Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la 1 Petulo 1 PETULO ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Moni (1, 2) Kubadwanso mwatsopano nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika (3-12) Mukhale oyera monga ana omvera (13-25) 2 Muzilakalaka Mawu a Mulungu (1-3) Miyala yamoyo ikumangidwa nʼkukhala nyumba yauzimu (4-10) Muzikhala ngati alendo mʼdzikoli (11, 12) Muzigonjera anthu oyenera kuwagonjera (13-25) Khristu ndi chitsanzo chathu (21) 3 Akazi komanso amuna apabanja (1-7) Muzimverana chisoni; muziyesetsa kumakhala mwamtendere (8-12) Kuvutika chifukwa chochita zinthu mwachilungamo (13-22) Muzikhala okonzeka kufotokoza za chiyembekezo chanu (15) Ubatizo komanso chikumbumtima chabwino (21) 4 Muzichita zimene Mulungu amafuna, ngati mmene Khristu ankachitira (1-6) Mapeto a zinthu zonse ayandikira (7-11) Kuvutika chifukwa chokhala Mkhristu (12-19) 5 Wetani gulu la nkhosa za Mulungu (1-4) Mukhale odzichepetsa komanso atcheru (5-11) Muzitula nkhawa zanu zonse kwa Mulungu (7) Mdyerekezi ali ngati mkango wobangula (8) Mawu omaliza (12-14)