Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la 1 Yohane 1 YOHANE ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Mawu opatsa moyo (1-4) Muziyenda mʼkuwala (5-7) Tiyenera kuvomereza machimo (8-10) 2 Yesu, nsembe yophimba machimo (1, 2) Kusunga malamulo ake (3-11) Lamulo lakale komanso latsopano (7, 8) Chifukwa cholembera kalatayi (12-14) Musamakonde dziko (15-17) Tichenjere ndi wokana Khristu (18-29) 3 Ndife ana a Mulungu (1-3) Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi (4-12) Yesu adzawononga ntchito za Mdyerekezi (8) Muzikondana (13-18) Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu (19-24) 4 Muzifufuza mawu ouziridwa (1-6) Kudziwa komanso kukonda Mulungu (7-21) “Mulungu ndi chikondi” (8, 16) Munthu wachikondi sachita mantha (18) 5 Amene amakhulupirira Yesu amagonjetsa dziko (1-12) Tanthauzo la kukonda Mulungu (3) Tizikhulupirira kuti pemphero ndi lamphamvu (13-17) Tizisamala mʼdziko loipali (18-21) Dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo (19)