Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la Oweruza OWERUZA ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Madera omwe Yuda ndi Simiyoni anagonjetsa (1-20) Ayebusi anapitiriza kukhala ku Yerusalemu (21) Yosefe anagonjetsa Beteli (22-26) Akanani ena anasiyidwa (27-36) 2 Chenjezo la mngelo wa Yehova (1-5) Imfa ya Yoswa (6-10) Oweruza anayamba kupulumutsa Isiraeli (11-23) 3 Yehova anayesa Aisiraeli (1-6) Otiniyeli, woweruza woyamba (7-11) Woweruza Ehudi anapha mfumu yonenepa Egiloni (12-30) Woweruza Samagara (31) 4 Mfumu Yabini ya ku Kanani inkapondereza Aisiraeli (1-3) Mneneri wamkazi Debora ndi woweruza Baraki (4-16) Yaeli anapha Sisera mkulu wa asilikali (17-24) 5 Nyimbo imene Debora ndi Baraki anaimba atapambana (1-31) Nyenyezi zinamenya nkhondo yolimbana ndi Sisera (20) Mtsinje wa Kisoni unasefukira (21) Okonda Yehova ali ngati dzuwa (31) 6 Amidiyani ankapondereza Aisiraeli (1-10) Mngelo anatsimikizira woweruza Gidiyoni kuti amuthandiza (11-24) Gidiyoni anagwetsa guwa lansembe la Baala (25-32) Mzimu wa Mulungu unathandiza Gidiyoni (33-35) Kuyesa ndi ubweya wa nkhosa (36-40) 7 Gidiyoni ndi anthu ake 300 (1-8) Asilikali a Gidiyoni anagonjetsa Amidiyani (9-25) “Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!” (20) Chipwirikiti mumsasa wa Amidiyani (21, 22) 8 Amuna a ku Efuraimu anakangana ndi Gidiyoni (1-3) Mafumu a ku Midiyani anathamangitsidwa nʼkuphedwa (4-21) Gidiyoni anakana ufumu (22-27) Mbiri ya Gidiyoni (28-35) 9 Abimeleki anakhala mfumu ku Sekemu (1-6) Mwambi wa Yotamu (7-21) Ulamuliro wankhanza wa Abimeleki (22-33) Abimeleki anapha anthu ku Sekemu (34-49) Mzimayi anavulaza Abimeleki ndipo anafa (50-57) 10 Oweruza Tola ndi Yaeli (1-5) Aisiraeli anasiya Mulungu kenako nʼkulapa (6-16) Aamoni anaopseza Aisiraeli (17, 18) 11 Woweruza Yefita anathamangitsidwa kenako anakhala mtsogoleri (1-11) Yefita anakambirana ndi Aamoni (12-28) Lonjezo la Yefita komanso mwana wake wamkazi (29-40) Mwana wa Yefita sanakwatiwe (38-40) 12 Anakangana ndi amuna a ku Efuraimu (1-7) Anawayesa ndi mawu akuti “Shiboleti” (6) Oweruza Ibizani, Eloni ndi Abidoni (8-15) 13 Mngelo anapita kwa Manowa ndi mkazi wake (1-23) Kubadwa kwa Samisoni (24, 25) 14 Woweruza Samisoni ankafuna mkazi wa Chifilisiti (1-4) Mzimu wa Yehova unathandiza Samisoni kupha mkango (5-9) Mwambi wa Samisoni pa ukwati (10-19) Mkazi wa Samisoni anaperekedwa kwa mwamuna wina (20) 15 Samisoni anabwezera Afilisiti (1-20) 16 Samisoni ku Gaza (1-3) Samisoni ndi Delila (4-22) Samisoni anabwezera nʼkufa (23-31) 17 Mafano a Mika ndi wansembe wake (1-13) 18 Anthu a fuko la Dani ankafufuza malo (1-31) Mafano a Mika ndi wansembe wake anatengedwa (14-20) Anagonjetsa Laisi nʼkusintha dzina kukhala Dani (27-29) Kulambira mafano ku Dani (30, 31) 19 Anthu a fuko la Benjamini anagwirira mkazi ku Gibeya (1-30) 20 Nkhondo yomenyana ndi fuko la Benjamini (1-48) 21 Fuko la Benjamini linapulumutsidwa (1-25)