Tsamba 2
Anthu alidi odera nkhaŵa umoyo lerolino, ndipo pali unyinji wosiyanasiyana wa zothandizira umoyo zosankhapo: masewera, kadyedwe, njira za mankhwala amakono. Komabe, mosasamala kanthu za unyinji wa ndalama zowonongedwera pa zinthu zimenezi, kodi tsopano tiri aumoyo moposerapo kuposa kumbuyoko? Kodi tingauchitirenji umoyo wathu? Kodi umoyo wokwinyirira udzalakidwadi?