“Lolimba Ngati Thanthwe la Gibraltar”
Lokwezeka m’mwamba pa utali wa mamita 426, kuchokera m’madzi obiriŵira a Mediterranean, Thanthwe la Gibraltar ndithudi limawoneka lolimba. Pa tsiku lowala, wina akhoza kuwona mosavuta nsonga ya Gibraltar kuchokera pa malo ozungulira pa mtunda wa makilomita angapo kumwera kwa Spain, ndi kuchokera ku Morocco, tsidya lina la Mediterranean.
Mbiri ya Gibraltar imabwerera kumbuyo kufika ku nyengo zamdima zija pamene amalinyero akale, akukhulupirira kuti dziko lapansi linali losalala, analingalira kuti kupyola m’Thamanda la Gibraltar kukawafikitsa kumalire a dziko ndi ku phompho la chiwonongeko. Linalingaliridwanso kukhala imodzi ya Mizati ya Hercules, winawo ukumakhala Jebel Musa ku Ceuta, ku malire a Africa tsidya lina la thamandalo. Nthano idanena kuti ngwazi Yachigriki Hercules anagawa mapiri pakati.
Mzinda wa Gibraltar unakhazikitsidwa ndi Aluya omwe anabwera kuchokera Kumpoto kwa Africa m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu C.E. ndipo pambuyo pake anayambitsa mzindawo mu 1160. Dzina lakuti Gibraltar linachokera ku Lachiluya lakuti Djabal-Tarik, kapena Phiri la Tarik. Ṭāriq ibn Ziyād anali mtsogoleri Wachiluya yemwe anagonjetsa mfumu yomalizira ya Goth mu 711 C.E.
Anthu Achispanya anagonjetsa Gibraltar mu 1462, kokha kudzalandidwanso ndi anthu a ku Britain mu 1704. Kufikira lerolino, lidakali imodzi ya malo akunja a Ufumu wakale wa Britain. Koma Thanthwe la Gibraltar likupitirizabe kukhala chizindikiro cha chinachake cholimba ndi chokhalitsa.
Mipingo iŵiri (Wachingelezi ndi Wachispanya) ya Mboni za Yehova 120 mu Gibraltar ikupereka lonjezo la Ufumu wa Mulungu kwa anthu a ku Gibraltar, lonjezo lolimbadi kuposa Thanthwelo!—Tito 1:1, 2; Ahebri 6:17-19.