Chochitika Chofunikira Kukumbukira!—Lachiŵiri, April 10
Panali pa Nisani 14 ya chaka cha 33 C.E. Yesu ankagaŵana chikho cha vinyo ndi mtanda wa mkate wopanda chotupitsa ndi atumwi ake. Malangizo ake? “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19. Chotero, kamodzi pachaka, Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zimakumana pamodzi kukumbukira imfa ya Yesu m’njira imene iye analangizira pa usiku umene anapanga ndemanga imeneyo. Chaka chino, Nisani 14 idzayamba pa Lachiŵiri, April 10, pa kuloŵa kwa dzuŵa. Mukuitanidwa mwamanja aŵiri kudzagwirizana nafe m’msonkhano wokumbukira umenewu madzulo a Lachiŵiri limenelo. Chonde fufuzani kwa Mboni za Yehova zakumaloko kaamba ka nthaŵi yeniyeni ndi malo a kukumanako.