Tsaganani Nafe Paulendo Wathu wa Pamtsinje wa Chobe
NDI MLEMBI WA GALAMUKANI! MU SOUTH AFRICA
TIRI m’bwato pa Mtsinje wa Chobe mkati mwenimweni mwa Kummwera kwa Afirika. Tchuti chathu chafika pachimake. Tikumva madzi akugavira pang’onopang’ono kumenya bwatolo pamene apaulendo ena akukwera. Pagombe, mabango akundenguma ndi yaziyazi wa mphepo yotilonjera. Ndife okondwera ndi mitambo imene ikutichinga kudzuŵa lotentha la mu Afirika.
“Ndikukhulupirira kuti njovu zidzadza masana ano kudzamwa madzi monga mwanthaŵi zonse,” akutero Jill, manijala wachikazi wolandira alendo wapa hotela amene amakonza ulendo woterewu. Ifenso tikukhulupirira choncho. Mtsinje wa Chobe ngwotchuka kaamba ka njovu zake. Kumpoto kwa Botswana, kumene malire ake ali pa Mtsinje wa Chobe, kuli pafupifupi njovu 45,000—kumene zinachuluka kuposa malo ena alionse kum’mwera kwa Afirika. “Komabe,” akuchenjeza Jill, “chifukwa cha mvula yaposachedwapa, sitinawone njovu kwa masiku atatu.”
Komabe, Mtsinje wa Chobe uli ndi zokopa zina zambiri. M’chotengera china m’bwatomo, tikuwona nsomba zinayi zakufa. “Nthaŵi zonse timapeza nkhwazi zikudikhirira kuti nsomba zitayidwe pamadzi,” akutero Rainford, kapiteni wabwato lathu waku Botswana. Kodi tidzapeza chipambano kujambula imodzi yambalame zimenezi pamene ikuthethula chakudyacho? Chidwi chathu chikukula pamene tiwona bwato lina la alendo, lotchedwa The Fish Eagle, likutipitirira. Bwato lathu likutchedwa Mosi-Oa-Tunya, dzina Lachifirika la Victoria Falls. Mtsinje wa Chobe umagwirizana ndi mtsinje wamphamvu wa Zambezi kumagwera pamathithi otchuka, amene ali pamtunda wa pafupifupi ola limodzi ndigalimoto kuchokera pano.
Mwawona nanga, mwamsanga Mosi atanyamuka, tikuwona njovu kupyolera m’mandala owonera patali. Komatu, kalanga ife, pamene tikadali kutali, izo zibwereranso m’thengo. “Kufikira milungu itatu yapitayo,” akukumbukira motero Sandy, wotsogoza ulendo wathu, “tinali kuwona nsambi yanjovu mazana ambiri.” Ndiyeno, chisamaliro chathu chikusumikidwa pa mingoma isanu ndi umodzi ikutiyang’ana kuchokera pagombe. Pamene galimoto liyandikira, kaŵirikaŵiri mingomayi imathawa mofulumira. “Siimawonekera kuchita mantha kwambiri ndi bwato pamadzi,” akutero Sandy.
Kuimba kokoma kwa njiŵa kukudodometsedwa ndi kulira kofuula kwambiri. Kodi ndimbalame yanji imeneyo? “Mfuu yomvekera bwino yankhwazi yamu Afirika njanthaŵi zonse mu Mtsinje wa Chobe,” akufotokoza motero Dr. Anthony Hall-Martin m’buku lotchedwa Elephants of Africa. Zinayi za mbalame zazikukulu zimenezi zikutiyang’anitsitsa kuchokera pa mitengo yondanda m’mphepete mwa mtsinjewo. Mwamsanga tikukonzekeretsa makamera athu pamene Sandy akuponya nsomba imodzi. Mofulumira, mbalame yoyamba ikuchoka panthambi yake niwulukira kwa ife. Chotsatira, tikumva khavaa, pamene nsombayo igwidwa mwamphamvu m’zikhadabo za mbalameyo. Kenaka, mwakukapira ndi mapiko ake aakuluwo, ikuwuluka kuchoka pamadzi ikumatulutsa mfuu yachilakiko—HOO-kiyoo-kwoo. Tikuchita kakasi ndi kugwirizana kwa maso, zikhadabo, mfuu, ndi mapiko zotsogozedwa ndi ubongo wochepa wa nkhwaziyo. M’bwatomo mwangoti zii, kusiyapo khetye-khetye wamakamera, pamene chochitika chochititsa chidwi chimenechi chikubwezeredwa nthaŵi zina zitatu.
Pamene bwatolo lipita patsogolo, tikuwona nsambi ya njovu 26, kuphatikizapo tiana, zikumaseŵera m’madzi. Kuziwonerera kukukumbutsa mawu a Bruce Aiken m’buku lake la The Lions and Elephants of the Chobe akuti: “Ludzu litatha, zazikulu zimaseŵera mwakumadzithirathira madzi ndi zitamba zawo. Zina, makamaka zocheperapo ndi zamphongo, zimakonda kuloŵa mumtsinjemo ndikumasambira moseŵera zikumazungulira m’madzi, kaŵirikaŵiri zikumangowoneka nsonga zokha zazitamba zawo pamwamba pamadzi monga timipaipi topumiramo. Komabe, tiana ndito tikusangalala koposa zonse. Uku ndiko kuyamba kwanthaŵi yakuseŵera, ndipo zikulumphalumpha ndi kuthamangitsana . . . Popeza kuti ludzu latha, tsopano ndinthaŵi ya chochitika china chosangalatsa, ndipo mosakaikira chokondedwa, kuseŵera m’thope. . . . Posapita nthaŵi, zazikazi zododometsa maseŵera zimene zimalamula, zisankha kuti nthaŵi yakupita yakwana.”
Mwachisoni, kufika kwa bwato lathu lalikulu losanjana kupangitsa “zazikazi zododometsazo” kuchita mantha, ndipo zitsogolera nsambiyo kuchoka, koma titajambula kale zithunzithunzi.
Tsikulo sirinathe, ndipo Mtsinje wa Chobe ukadali ndi zodabwitsa zina. Chifukwa cha fumbi lochokera ku Chipululu cha Kalahari, kuloŵa kwadzuŵa patsidya lamtsinjewo nkosangalatsadi. Madzulo alinso nthaŵi pamene mvuu zaulesizo zimayamba kutakasuka pamene zikonzekera kuvuuka m’madzi kuti zikabudule udzu usiku. Panopa kusungika kwa bwato lathu lalikulu nkotsimikizirika. “Mungayandikire pafupi ndi mvuu mosachita mantha,” akutero Rainford.
Kubuma kwamphamvu, kukutidziŵitsa kuti tayandikira padziŵe la mvuu limene liri m’mphepete mwachisumbu mumtsinjemo. Umodzi pambuyo paunzake, mitu yaikulu ya mvuu ikuwonekera kumbali zathu zonse ziŵiri. Mwadzidzidzi, mvuu ziŵiri ziyamba kukankhana zitaasama kwambiri kukamwa—makamwawo ngaakulu mokwanira kubwathamamo munthu. Kenaka, mvuu ina ikubwera motilunjika, kuchokera pamadzi osaya pafupi ndi chisumbucho—niifika pafupi kwambiri kotero kuti thupi lake lalikululo lidzaza maleni a makamera athu. Pamene ifika pamadzi akuya kwambiri, mutu wake umira, ikumasiya msana wake waukuluwo ukuwonekera pamwamba. Ndiyeno, mwakutulutsa mpweya kuchokera m’mapapu, thupi lonse lalikululo limira.
Tikudabwa kumva kuti mosasamala kanthu za kulemera kwake kofika matani anayi, mvuu njopepuka thupi kwambiri m’madzi. “Ingasambire paliŵiro lalikulu kuposa nsomba zina zambiri mosasamala kanthu za chithupi chake chachikulu ndipo kaŵirikaŵiri mungayiwone m’madzi oyera ikusambira mothamanga chapamwamba,” akutero Bradley Smith m’buku lake lakuti The Life of the Hippopotamus. Kapena zitafuna, mvuu zimavina ndi miyendo yawo yamphamvu panthaka yapansi pamtsinje wakuya. Kuli monga momwe Mlengi wamunthu akunenera kuti:
“Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe, ikudya udzu ngati ng’ombe. Tapenya tsono, mphamvu yake iri mchiuno mwake, ndi kulimbalimba kwake kuli m’mitsepha ya m’mimba yake. Tawona madzi a mtsinje akakula, siinjenjemera; irimbika mtima, ngakhale Yordano [Mtsinje] atupa mpaka pakamwa pake.” (Yobu 40:15, 16, 23. Pokhala ozingidwa motere ndi zitsanzo za “mphamvu yake” zimenezi, timazindikira kufunika kwakukulu kwa kusonyeza ulemu kwa Amene anazipanga. “Ikakhala maso, munthu adzaigwira kodi? Kapena kuboola m’mphuno mwake iri m’khwekhwe?” akufunsa motero Yehova Mulungu, akumatikumbutsa zakupereŵera kwathu kwaumunthu.—Yobu 40:24.
Titagawanika maganizo, pakati pa kuwonerera kuloŵa kwa dzuŵa kwaulemerero ndi mvuu imeneyo, tikuzengereza kuchoka pamene nthaŵi ikwana yakuti bwato lathu libwerere. Pambuyo pake, titakhala m’nyumba yathu yaudzu m’mphepete mwa mtsinjewo, tikuwonerera mozizwa pamene thambo lisandulika m’mitundu ya upofu ndi kuyezuka, mawonekedwewo akupenyerereka mokongola m’madzi. Tikusinkhasinkha pazinthu zokondweretsa zimene tawona ndi kuzimva. “Ngati mufunadi kuyandikana ndi nyama zakutchire,” akutiuza motero Sandy, “muyenera kugwiritsira ntchito bwato laling’ono la injini.” Tikusankha kulabadira uphungu wake ndi kuchita haya bwatolo kaamba ka masana a tsiku lotsatira.
Panthaŵi ino, tikuyandikiradi pafupi ndi nyama zakuthengo, kusiyapo mvuu yowopsayo, ndipo tikhoza kugwira ngakhale mabango ndi akakombo apamadzi. Tikuwonereranso mbalame zogwira nsomba pamene zikudendekera malo amodzi mumlengalenga pamwamba pamadzi kufunafuna nsomba zing’ono. Mbalame zina zamaanga okongola zikuuluka motizungulira, zodya nsomba, zodya njuchi, ndi anamzeze aang’ono amaŵanga. Kenaka, pali mbalame zazikulu zokonda kukhala pazisumbu za mtsinje kupeza chitetezo—Atsekwe, ajacana, acormorant, ndi akakoŵa, kungotchulapo zoŵerengeka. Tikupitirira mtengo wina womira mbali imodzi wokometseredwa ndi mbalame zimenezi.
Pomalizira pake, tikufika pamalo amene tidawonapo nsambi ya njovu dzulo. Koma tsopano tikupezapo chiyendayekha (njovu yamphongo) amene akutinyalanyaza napitirizabe kudya ndikumwa. Ndiyeno, pamene tiyamba kunyamuka, mwadzidzidzi mayi ndi tiana asokoloka kuchokera pathengo. Mayiyo akuzengereza atatiwona. Tangokhala chete moyembekezera. Kodi adzabwerabe kapena ayi? Mwamwaŵi, akusankha upandu wa kulola ana ake kutulukira kwa ife. Nkosangalatsa chotani nanga kuwona mayi, yocheperapo, ndi kamwana zikuthamanga motilunjika!
Aiken akupereka ndemanga yowonjezereka iyi m’buku lake ponena za mikango ndi njovu kuti: “Mungayerekezere ukulu wa ludzu limene nyama zazikulu zimenezi zimakhala nalo tsiku lirilonse . . . mwakuwona ulendo wautali ndi wotopetsa umene zimayenda kudzafika kumtsinjeko. Zikuyenda mwachangu ndipo mofulumira monga momwe zingathere, njovu zimasokoloka pathengo ndikulunjika mwaliŵiro pamalo omwera, kaŵirikaŵiri zikumathamanga kwadzawoneni mtunda wotsala wa mamita makumi asanu kapena zana limodzi zitanunkhiza madzi opatsa moyo.” Ndithudi, tikuwonerera mozizwa pamene zitatuzo zikundanda ndi kumwa, kamwanako kataikidwa pakati mokatetezera. Komatu nthaŵi ikupita, ndipo tiyenera kubwerera kusanade.
Kuwonjezera pa njovuzo, tikuwona njati, ng’ona, agwape, mingoma, anakhodze, achoŵe, anyani, ndi minjiri. Sitingachitire mwina kusiyapo kukhala oyamikira kwambiri kwa Uyo amene analenga nyama zakuchire zamitundumitundu zosangalatsa zimenezi ndi amene anaziika m’malo okongola otereŵa. M’nyengo yachirimwe, mbalame ndi nyama zimasonkhana kumtsinjeko m’magulu aakulu, ndipo ngakhale mikango, anyalugwe, zipembere zimapezeka.
Mwinamwake mukukhala kutali ndi mbali yakutali ino ya Afirika, koma tikukhulupirira kuti mwakutsagana nafe paulendo wathu, tsopano mwakhala ndi lingaliro labwinopo la zinthu zozizwitsa zoyembekezera kuwonedwa ndi amene ayenda pamtsinje wa Chobe.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
Zosemedwa zamtengo zonse: Nyama: 1419 Copyright-Free Illustrations of Mammals, Birds, Fish, Insects, etc. zakonzedwa ndi Jim Harter