Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 6/8 tsamba 31
  • “Agalu Auchiwanda”?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Agalu Auchiwanda”?
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Galu Wanu Sangavulaze Ana?
    Galamukani!—1997
Galamukani!—1992
g92 6/8 tsamba 31

“Agalu Auchiwanda”?

KULUMIDWA ndi agalu otchedwa pit bull m’Canada, Mangalande, ndi United States kunafalitsidwa kwambiri m’zaka zingapo zapitazo. Bungwe la Centers for Disease Control la ku United States linapereka lipoti lakuti 42 peresenti ya imfa zokwanira 157 zochititsidwa ndi kulumidwa ndi agalu mu United States pakati pa 1979 ndi 1988 zinali zakulumidwa ndi agalu a pit bull. Ku Briteni ofalitsa nkhani amatcha agalu a pit bull olusa amenewo “Agalu Auchiwanda.” Magazini a Equinox amatcha galuyo “makina akupha owopsa.”

Pochita maseŵera osaloledwa omenyanitsa agalu, pit bull amanenedwa kukhala “ngwazi yakupha,” chifukwa cha nyonga yake, kupepuka thupi, kulimba mtima, ndi nkhalwe. Magazini a The Globe and Mail a ku Toronto, Canada, amanena kuti ‘pit bull amaŵetedwera kuphera agalu ena.’

“Mano ake olimba akuthwa akhoza kuvulaza mowopsa nyama zina ndi anthu, makamaka ana, osakhoza kudzichinjiriza,” akutero magazini a The Toronto Star. Nkhani zochititsa chisoni za kulumidwa zimaphatikizapo mtsikana wazaka zisanu ndi zinayi yemwe anapangidwa opareshoni ya maola asanu yakumuika minofu ina kunkhope m’mbali zomwe anazomoledwa ndi galu wa pit bull. Mwana wina wazaka 13 anafunikira chithandizo chakuchiritsidwa pamene anazomoledwazomoledwa kunkhope, m’thupi, m’miyendo, m’ntchafu, ndi m’matako. Wosonyeza kukongola wazaka 21 anakhazulidwa mowopsa kunkhope pamene ankayesa kupsompsona galu wa bwenzi lake wa pit bull, kotero kuti anasokedwa mfundo 70. Ku Mangalande, mwamuna wa zaka 54 anakhazulidwa ndi “Agalu Auchiwanda” aŵiri ndipo mphuno yake inazomoledwa.

Kathleen Hunter, mtsogoleri wamkulu wa Toronto Humane Society, kale ankakhulupirira kuti mutamphunzitsa bwino, galu wa pit bull akhoza kukhala chiŵeto mofanana ndi agalu ena. Komabe, tsopano akuvomereza kuti “galu wa pit bull ali ndi mkhalidwe winawake m’majini umene umampangitsa kukhala nyama yokaikiritsa kwambiri. Alidi galu wolusa . . . , amene amaluma ngakhale pamene sanaputidwe.”a Manijala wamkulu wa nthambi yoyang’anira zinyama ya Toronto’s Public Health Department, Jim Bandow, ananena kuti: “Galu wa pit bull ali ngati bomba la nthaŵi. Simungadziŵe pamene lidzaphulika.”

Opanga malamulo akuyesa kuthetsa vutolo mwakupereka malamulo osiyanasiyana. Osunga agalu a pit bull mu Edmonton, Canada, ayenera kukhala ndi ndalama za inshuwalansi zosachepera pa $500,000 kaamba ka mlandu umene ungabuke ndipo amalipira $100 ya laisensi. Mu Winnipeg, Canada, agalu a pit bull atsopano samaloledwa m’tauni, ndipo eni ake ayenera kuika kuunyolo agalu awo ndi kuwamanga kukamwa ndi kusonyeza $300,000 ya inshuwalansi ngati pangagwe mlandu. Nyumba Yamalamulo ya ku Briteni inapereka malamulo ofanana kwa osunga agalu a pit bull. Amene amaswa malamulo a Briteni amalipiritsidwa faindi ndi kuponyedwa m’ndende.

Malinga ndi Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli wakale, nyama zolusa zinayenera kuyang’aniridwa. Ngati nyama yolusa inamasuka, mwiniwake anakhala ndi mlandu wa chivulazo chimene inachita. Ngati nyamayo inapha munthu, mwiniwakeyo anakhala ndi liwongo la mwazi, ndipo zimenezo zikamtaitsa moyo wake. (Eksodo 21:29) Polingalira zimene zinalembedwa m’Chilamulo cha Mulungu, kungakhale kwanzeru kwa Akristu kutsatira njira zofunikira kotero kuti achinjirize agalu olusa ndi okaikiritsa, kapena kusawaŵeta konse.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mumve zochuluka pankhaniyi, onani Awake! ya March 22, 1988, tsamba 25.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena