Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?
Funso lokopa maganizo limeneli ndilo mutu wankhani wa trakiti limene limagaŵiridwa ndi Mboni za Yehova. Chaka chatha munthu wina, nzika ya Washington, D.C., analandira trakiti limeneli nanena kuti anachita nalo chidwi. Iye analemba kuti:
“Kuli koonekeratu kwa aliyense wokhala m’likulu la dziko lathu kuti dziko lapansi likufikadi kumapeto. Northern Ireland, Yugoslavia wakale, malipabuliki akale a Soviet Union, onsewo akuchitira umboni wa mdima ndi mkangano zimene zakantha dzikoli lerolino. Ndende zosefukira ndi anthu, miliri yatsopano ya chifuŵa cha [TB] ndi chaola cha black plague, zonsezo zikutsimikizira mfundo imene mukufotokoza mu trakiti lanu.”
Mwamunayo anapempha kuti: “Chonde nditumizireni mawu owonjezereka ponena za lingaliro lanu lapadera, ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere limene mumapereka.”
Mboni za Yehova zimasonyeza anthu zimene Baibulo limanena ponena za mtsogolo mwa mtundu wa anthu. Ngati mungafune kope la trakiti lotchulidwa pamwambapa kapena phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pa ndandanda ya patsamba 5.