Kodi Tikumka Kuti?
TAYEREKEZERANI kuti mukuyenda kupyola m’dera limene simunaonepo. Pakali pano mukanayenera kukhala mutafika kumene mukupita, komano zizindikiro za m’msewu, maina a matauni, ndi zizindikiro zina za malo sizili zimene munayembekezera. ‘Kodi ndili kuti?’ inu mukudabwa motero. ‘Kodi ndatenga njira yolondola?’
Dziko la lerolino lili mu mkhalidwe wofananawo. Munthu wafika m’dera limene salidziŵa pamene akuona makhalidwe a anthu akuipa pa mlingo umene sunaonedwepo ndi kale lonse. Limodzi ndi kupita patsogolo m’zasayansi ndi m’luso la zopangapanga, kukuonekera ngati kuti patsopano lino tikanayenera kukhala m’dziko labwinopo. Mu Great Ages of Man, mkonzi Russell Bourne akunena kuti ndi m’zaka za zana la 20 mokha mmene “lingaliro lakale la ubale wa padziko lonse linaoneka kukhala lotheka kwambiri.”
Komabe, malo amenewo amene “ubale wa padziko lonse” ukupitako aphonyedwa. Zizindikiro zolonjezedwazo za chisungiko cha chuma, chakudya chokwanira, thanzi labwino, ndi moyo wa banja wachimwemwe sizikupezeka. “M’njira zambiri,” buku lakuti Milestones of History likutero, “kupita patsogolo kwa sayansi kwagwirizanitsidwa mwachindunji ndi kuwononga ndi nkhanza.”
Inde, lerolino anthu asokera m’dera lachilendo, lokhala kutali ndi njira yolondola, kutali ndi mtendere ndi chisungiko zimene zinaonedwa pa kuyambika kwa zaka za zana lino. Motero, lerolino ambiri akufunsa za njira yolondola: “Kodi tinaloŵa bwanji mu mkhalidwe umenewu? Kodi dzikoli likumka kuti? Kodi tikukhala m’masiku otsiriza?”
Kuti tidziŵe pamene tili, choyamba tiyenera kudziŵa kumene tili tsopano lino. Ena amanena kuti tili pakhomo penipeni pa dongosolo la dziko latsopano; ena amati tili pamphembenu penipeni pa chiwonongeko. Baibulo, monga mapu a msewu, limatithandiza kuona pamene kwenikweni tili ndi kumene tikumka.
Pamene mukuyenda ulendo, kuli kofunika kuyang’anitsitsa zizindikiro zimene zidzasonyeza malo anu. Mofananamo, Baibulo limafotokoza za mbali—mikhalidwe ya dziko ndi mikhalidwe ya maganizo—zimene zikasonyeza nyengo ina m’mbiri yotchedwa “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Mawu ameneŵa, akuti “masiku otsiriza,” samanena za kutha kwa miyamba yeniyeni ndi dziko lapansi lenileni. M’malo mwake, amasonyeza za “[mapeto a dongosolo la zinthu, NW ]” kapena “mapeto a nyengo,” monga momwe matembenuzidwe ena a Baibulo amanenera.—Mateyu 24:3; Today’s English Version.
“Masiku otsiriza,” mtumwi Wachikristu Paulo analemba motero, “zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Zoonadi, zimenezi zingaonekerenso ngati kuti zikunena za nyengo zina za mu mbiri. Ndithudi, nyengo iliyonse yakhala ndi mavuto ake.
Nangano, kodi pali chifukwa chotani cha kukhulupirira kuti mawu ameneŵa amanena za tsiku lathu?
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Tom Haley/Sipa Press