Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 9/8 tsamba 32
  • Mtsogolo Mwabwino Kwambiri mwa Pulaneti la Dziko Lapansi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtsogolo Mwabwino Kwambiri mwa Pulaneti la Dziko Lapansi
  • Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 9/8 tsamba 32

Mtsogolo Mwabwino Kwambiri mwa Pulaneti la Dziko Lapansi

“KUFUFUZA kukusonyeza kuti Dziko Lapansi tsopano lili lofunda kwambiri kuposa mmene lakhalira m’zaka 600,” ikutero Globe and Mail ya ku Toronto. Mu 1995 mpweya wotentha cha pakati pa United States unapha anthu oposa 500 mu Chicago. Mikhalidwe yofananayo yoipa kwambiri inachitika ku India ndi Australia, pamene kuli kwakuti England anakhala ndi “chilimwe chachitatu chouma koposa m’zaka 200.”

Kodi nchiyani chikuchititsa zimenezi? Henry Hengeveld, wa mu Environment Department ya boma ku Canada, wodziŵa za mkhalidwe wa dziko, akuti: “Umboni wochuluka ukusonyeza kuti pali chiyambukiro choonekera cha anthu pa mkhalidwe wa dziko lonse.” Malinga ndi lipoti la Globe and Mail, “machedwe achilendo akufanana ndi zosonyezedwa pa makompyuta amene amasonyeza zotulukapo za kutentha kwa dziko lonse, kumene amati kukuchititsidwa makamaka ndi kutentha mafuta.”

Kunena kuti dziko lonse likutentha ndi nkhani imene asayansi akali kusiyanapo malingaliro. Ngakhale zili choncho, The New Encyclopædia Britannica ikunena kuti: “Anthu akuwononga mlengalenga mwamsanga kuposa ndi mmene akuumvetsetsera.”

Mwaŵi wake ngwakuti, Baibulo limatiuza kuti dziko lapansi “lingokhalabe masiku onse.” (Mlaliki 1:4) Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti Mlengi, Yehova Mulungu, sadzalola munthu kapena mphamvu iliyonse yachilengedwe kuliwononga. M’malo mwake, iye ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:17, 18.

Ndiponso, Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova Mulungu wasungira pulaneti lathu la Dziko Lapansi ndi anthu onse omvera mtsogolo mwabwino kwambiri. “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Tili achimwemwe kotani nanga kuti mtsogolo mwa dziko lapansi muli m’manja mwa Mulungu, osati mwa munthu!—Salmo 37:11; 72:16; Yesaya 65:17-25; 2 Petro 3:13.

Ngati mukufuna kulandira makope a mtsogolo a Galamukani!, chonde onanani ndi Mboni za Yehova zakwanuko kapena lemberani ku keyala yapafupi kwambiri ndi kwanu yondandalitsidwa patsamba 5.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Chithunzi cha NASA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena