Linamsonkhezera Kuchitapo Kanthu!
Mwamuna wina wa ku Caracas, likulu la Venezuela, anakachezera atate wake okalamba, a Rufino. Atate wakewo ankakhala ku La Loma, kumudzi wakutali. Iye anatengera Rufino buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.
Pambuyo pake, Mboni za Yehova za ku Los Humocaros zinakalalikira ku La Loma. Zinadabwa kwambiri kumva anthu akuwauza kuti Mboni ina inali kuwachezera. Mbonizo zinazizwa chifukwa zinadziŵa kuti kudera limenelo kunalibe Mboni iliyonse. Ndiye wina anazisonyeza munthuyo yemwe amati ndi Mboni—inali nyumba ya Rufino imeneyo!
Rufino anakondwera kwambiri kuonana ndi alendo ake. Nanga nchifukwa ninji anthu apamudzi pakepo ananena kuti iye anali mmodzi wa Mboni za Yehova? Chabwino, Rufino anayamba kuŵerenga buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, ndipo atafika pamutu 13, anaona chithunzithunzi cha Yesu akutumiza otsatira ake kuntchito yolalikira. Rufino anaganiza kuti Akristu lerolino ayenera kuchita ntchito imodzimodziyo. Choncho anayamba kuuza anansi ake za choonadi cha Baibulo chimene anali kuphunzira.
Phunziro la Baibulo lokhazikika linayambika ndi Rufino, ndipo anamuuza za misonkhano ya mpingo. Sande yotsatira anafika pa Nyumba ya Ufumu. Ngakhale kuti Rufino anali ndi zaka 80, anayenda maola atatu kuti adzapezekepo! Kuyambira tsiku lomwelo, sanaphonyepo msonkhano uliwonse pokhapo atadwala kwambiri. Analembetsa ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki yomwe nakamba nkhani yabwino. Chaka chatha Rufino anadwala ndipo anamwalira m’July 1996, ali ndi chiyembekezo cholimba cha kuuka kwa akufa m’dziko lapansi la paradaiso.
Tikhulupirira kuti inunso mudzapindula mwa kuŵerenga buku lamasamba 256 lazithunzithunzi zokongola lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ngati mukufuna kulandira kope lake kapena ngati mukufuna kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena kukeyala yoyenera patsamba 5.