Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 11/8 tsamba 32
  • Amaikondadi Nsanja ya Olonda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amaikondadi Nsanja ya Olonda
  • Galamukani!—1997
Galamukani!—1997
g97 11/8 tsamba 32

Amaikondadi Nsanja ya Olonda

“Ngakhale kuti ndine wa Roma Katolika,” analemba motero wophunzira wa giredi sikisi wa ku Toledo, Ohio, U.S.A., “ndikufuna kulembetsa sabusikripishoni ya magazini yanu. Ndinachita chidwi ndi Nsanja ya Olonda chifukwa cha Trevor. Iyeyo amakhala ndi ine m’kalasi. Takhala mabwenzi pafupifupi chaka chimodzi tsopano, ndipo wandiphunzitsa zambiri ponena za Yesu, Yehova, ndi Mboni za Yehova.

“Zaka za Trevor zifanana ndi zanga, msinkhu wake ndiye msinkhu wanga, ndipo ngwodzipereka kwambiri pa chipembedzo chake. Ali ndi sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda ndipo amandibwereka magazini ake. Ndimakonda nkhani zanzeru zomwe mumalemba. Ndikhulupirira kuti simudzayang’ana pamfundo yakuti sindine wa Mboni za Yehova ndipo mudzandilola kukhala ndi sabusikripishoni ya magazini yanu.”

Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake, Galamukani!, imaŵerengedwa ndi anthu a mafuko ndi zipembedzo zambiri padziko lonse lapansi. Chaka chatha chokha makope oposa mamiliyoni 900 a magazini aŵiri ameneŵa anasindikizidwa m’zinenero zoposa 120!

Inunso mungapindule mwa kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthaŵi zonse. Ngati mukufuna kulandira kope kapena kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena kukeyala yoyenera imene ili patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena