N’zotheka Kukhala ndi Banja Losangalala!
MAYI wina wokhala mumzinda wa Maladzyechna, ku Belarus, analemba kalata yopita ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Russia. Iye ananena kuti ngokwatiwa ndipo ali ndi ana aŵiri. Iye anati: “Ine ndi mwamuna wanga timakondana. Komabe ndinayamba kuona kuti titakhala limodzi kwa nthaŵi yaitali tinayamba kumangokwiyirana zilizonse n’kumangokangana popanda chifukwa chenicheni. Miyezi ingapo yapitayo munthu wina anandiimitsa ndili pamsewu n’kundipatsa kathirakiti kakuti Sangalalani ndi Moyo Wabanja. Poyamba chinandichititsa chidwi ndi chithunzi chokongola chosonyeza banja losangalala. Kenaka ndinaŵerenga nkhaniyo n’kumupatsa mwamuna wanga kuti naye aŵerenge.
“Banja lathu linasintha kwambiri, kungokhala ngati kutulo. Panopo timadziŵa kuti kukhala osangalala si chinthu chovuta kwenikweni. Chofunika ndicho kungokhala munthu wosonyeza chikondi chochokera pansi pamtima ndiponso wowoloŵa manja. M’pofunika kutsatira malamulo a Mulungu m’moyo mwathu, kum’konda Mulungu ndi kukondanso anthu, kuphatikizapo achibale athu ngakhalenso anthu ena.”
Iye anamaliza n’kunena kuti: “Panopo moyo tinayamba kuumva kukoma kwabasi. Tikufuna kupitiriza kuphunzira Baibulo ndiponso kuphunzitsa ana athu.”
Tikukhulupirira kuti inunso mungathandizidwe ndi thirakiti imeneyi yakuti Sangalalani ndi Moyo Wabanja. Tingasangalalenso kukutumizirani buku la masamba 192 lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Kuti mulandire thirakitiyi ndiponso bukuli, chonde lembani zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni thirakiti yakuti Sangalalani ndi Moyo Wabanja ndi buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.