Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 34 tsamba 139-142
  • Kulambira Nkwa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulambira Nkwa Mulungu
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Wako Ndani?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Sakanagwada
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Chikhulupiriro Chawo Chinapulumuka Chiyeso Choopsa
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Anakana Kulambira Fano
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 34 tsamba 139-142

Mutu 34

Kulambira Nkwa Mulungu

INE ndidzakufunsani inu funso lofunika. Ilo liri lofunika kwambiri chakuti njira imene muyankhira imauyambukira moyo wanu wamtsogolo. Kodi Mulungu wanu ndani?—

Mulungu wanu ndiye amene inuyo mumamlambira. Anthu pa dziko lonse lapansi amalambira mitundu yambiri ya milungu. Ina ya milungu imeneyo iri chabe yosemedwa kapena yopangidwa ndi mtengo kapena mwala. Ina iri anthu ochuka kwambiri m’masewera kapena nyimbo. Iwo amachedwa kukhala “nyenyezi” ndi “mafano.” Koma kodi kuli koyenera kupereka ulemelero kwa milungu ina imeneyi?—

Mphunzitsi Wamkuruyo anati: “Ndiye Yehova Mulungu wako amene uyenera kumlambira, ndipo ndiko kwa iye yekha uyenera kuperekako utumiki wopatulika.”—Mateyu 4:10, NW.

Chotero Yesu anakumveketsa bwino lomwe. Kulambira kwathu nkwa Yehova Mulungu yekha. Ife sitingathe kupereka ngakhale kulambira kwathu kwapang’ono kwa mulungu wina ali yense. M’Baibulo muli nkhani ina yokondweretsa kwambiri yonena za anyamata ena amene anachidziwa chimenechi.

Maina ao anali Sadrake, Mesake ndi Abedinego. Iwo anali Ahebri, koma iwo anakhala m’dziko la Babulo. Mfumu ya Babulo inamanga fano lalikuru lagolidi. Iyo inalamulira kuti pamene nyimbo zinayimbidwa, munthu aliyense ayenera kugwadira fano lache. ‘Ali yense amene sagwada ndi kulambira pa nthawi yomweyo adzaponyedwa m’ng’anjo yamoto woyaka,’ iye anachenjezeratu. Kodi inuyo mukadachitanji?—

Sadrake, Mesake ndi Abedinego masiku onse anachita chiri chonse chimene mfumu inawalamulira. Koma iwo anakana kuchita chimenechi. Kodi mukuchidziwa chifukwa chache?—Chiri chifukwa chakuti lamulo la Mulungu linati: ‘Musakhale ndi milungu ina iri yonse kuphatikiza pa ine Musadzipangire nokha fano losema ndi kuligwadira ilo.’ Chotero Sadrake, Mesake ndi Abedinego anamvera lamulo la Yehova koposa lamulo la mfumuyo.—Eksodo 20:3, 4.

Mfumuyo inali yokwiya kwambiri pamene iyo inamva za chimenechi. Pomwepo inalamulira kuti Sadrake, Mesake ndi Abedinego abweretsedwe pamaso pache. Iyo inafunsa kuti: ‘Kodi ziri chonchodi kuti inu simuli kumaitumikira milungu yanga ya ine? Ndidzakupatsani mwai wina. Tsopano, pamene mumva nyimbo, gwadani ndi kulambira fano limene ine ndalipanga. Ngati simutero, mudzaponyedwa m’ng’anjo yamoto woyaka. Ndipo kodi mulungu ameneyo ndani amene angathe kukulanditsani inu m’manja mwanga?’

Kodi nchiani chimene Sadrake, Mesake ndi Abedinego akadachichita tsopano? Kodi nchiani chimene inuyo mukadachichita?—Iwo anadalira mwa Yehova. Iwo analankhula pomwepo nati kwa mfumuyo: ‘Mulungu wathu amene ife tiri kumamtumikira ali wokhoza kutilanditsa ife. Koma ngakhale ngati iye satilanditsa, milungu yanu sindiyo imene ife tidzaitumikira. Ife sitidzagwadira fano lanu la golidi.’

Mfumuyo inapsya mtima kwambiri. Iyo inalamulira kuti: ‘Ng’anjoyo itenthetsedwe kasanu ndi kawiri kutentha kwache koposa kwa masiku onse!’ Iyo inawalamulira anthu ache amphamvu kummanga Sadrake, Mesake ndi Abedinego. Ndiyeno iyo inati: ‘Aponyeni iwo m’ng’anjoyo!’

Atumiki a mfumuyo anawaponyeramo iwo. Koma ng’anjoyo inali yotentha kwambiri chakuti anthu ache a mfumuyo anaphedwa ndi malawi! Bwanji ponena za Ahebri atatuwo?

Sadrake, Mesake ndi Abedinego anagwera m’kati mwenimweni mwa motowo. Koma kenako iwo anadzuka! Iwo sanabvulale. Ndipo iwo sanakhalenso omangidwa. Kodi chimenechi chikadakhala chothekera motani?

Mfumuyo inayang’ana m’ng’anjoyo, ndipo chimene iyo inachiona chinaipangitsa iyo kuchita mantha. ‘Kodi ife sitinaponye amuna atatu m’moto?’ iyo inafunsa.

Atumiki ache anayankha kuti: ‘Inde, O mfumu.’

Koma mfumuyo inati: ‘Taonani ine ndikuona amuna anai akumayendayenda m’menemo, ndipo moto suli kumamuocha ali yense wa iwo.’

Kodi inu mukumdziwa amene anali munthu wachinaiyo?—Anali mngelo wa Yehova. Ndipo iye anali m’menemo kuwachinjiriza atumiki atatu okhulupirika Achihebri amenewo a Mulungu woona.

Poona ichi, mfumuyo inadza ku khomo kwa ng’anjoyo nipfuula kuti: “Sadrake, Mesake ndi Abedinego, atumiki a Mulungu Wam’mwambamwamba inu, turukani ndipo idzani pano!” Pamene iwo anaturuka, munthu ali yense adatha kuona kuti iwo sadaochedwe. Panalibe ngakhale pfungo la moto pa iwo.

Pamenepo mfumuyo inati: ‘Wodalitsika akhale Mulungu wa Sadrake, Mesake ndi Abedinego amene anawapulumutsa atumiki ache, chifukwa chakuti iwo sakadalambira konse mulungu wina ali yense kusiyapo Mulungu wao wa iwo eni.—Danieli chaputara chachitatu.

Kodi chimenecho sichinali chodabwitsa?—Yehova anakondwera ndi chimene anyamata atatu amenewo anachichita. Ndipo ife tingathe kuphunzira phunziro kuchokera mu icho.

Ngakhale lero lino anthu amaimika mafano kuti alambiridwe. Ena amapangidwa ndi mtengo kapena mwala kapena chitsulo. Kodi inuyo mukawagwadira mafano amenewa?—

Mafano ena apangidwa ndi nsaru. Kodi inu munayamba mwauona mtundu umenewo wa fano?—Kodi mukuganiza kuti ilo limapanga kusiyana kwa Mulungu ngati ilo lapangidwa ndi nsaru kapena ndi mtengo kapena mwala?—Kodi kukanakhala koyenera kaamba ka mtumiki wa Yehova kuchita kachitidwe ka kulambira pamaso pa fano loterolo?—

Sadrake, Mesake ndi Abedinego akadapereka kulambira kokha kwa Yehova. Mulungu anakondwera nawo. Kodi inu mudzachitsanzira chitsanzo chao?

(Awo amene amamtumikira Yehova sangawalambirenso mafano. Werengani chimene chanenedwa ponena za chimenechi pa Yesaya 42:8 ndi Yoswa 24:14, 15, 19-22.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena