Mutu 45
Mmene Timuuzira Mulungu Kuti, ‘Ndimakukondani’
KODI INU munadziwa kuti munthu wina anakukondani inu ngakhale pamene inuyo munali musanabadwe?—Eya, ndiyenera kukuuzani inu kuti ife tinadziwa kuti inu munalinkudza. Ndithudi, ife sitinadziwe kuti inu mudzakhala otani pa nthawi imeneyo. Inu munali kumakulabe m’mimba mwa mai wanu. Koma pa nthawi imeneyo atate wanu ndi mai wanu analinkumachita zinthu zambiri kusonyeza kuti iwo anakukondani inu.
Ndicho chifukwa chache kunali zobvala kuti inu mubvale mwamsanga pamene inu munabadwa. Ndipo kunali bedi laling’ono kuti inu mugonemo.
Ndipo, maine, ndi achimwemwe chotani nanga mmene atate ndi amai anu analiri pamene iwo potsirizira pache anakuonani inu! Iwo anakukondani pa nthawi imeneyo. Ndipo iwo amakukondani tsopano, kwambirimbiri. Inunso, mumawakonda atate ndi mai wanu, ati?—
Koma tsopano ine ndiri kumaganizira za munthu winanso ameneso anakukondani inu pamene inu munali musanabadwe. Kodi inu mukumdziwa ameneyo?—Ndi Yehova Mulungu. Kunena zoona, Mulungu anatikonda tonsefe pamene ife tinali tisanabadwe. Kodi inu mukudziwa mmene ife tikudziwira kuti iye anatikonda?—
Chifukwa chakuti kalekale Mulungu anamtumiza Mwana wache kudzaupereka moyo wache kaamba ka ife. Ndiponso, Mulungu adzalipangitsa dziko lapansi kukhala munda wokongola m’mene ife tingathe kukhalamo ndi moyo kosatha m’chimwemwe, ngati ife tikufunadi.
Kodi ndi motani mmene chimenechi chimakupangitsirani inu kulingalira kulinga kwa Mulungu?—Chimandipangitsa ine kumkonda iye kwambirimbiri. Ine ndikufuna kumtumikira iye moyo wanga wonse. Kodi nanu mukufuna?—
Koma kodi ndi motani mmene ife tingamuuzire Mulungu zimenezo?—Yesu anadziwa kumuuza kwache Mulungu zimenezo. Mvetserani pamene ine ndikukuuzani chimene iye anachita.
Tsiku lina iye anapita ku Mtsinje wa Yordano. Yohane Mbatizi anali komweko. Yesu ndi Yohane anayenda kubvu-kubvu kulowa m’madzimo. Madziwo anafika m’ziuno zao. Kodi inu muli ndi lingaliro liri lonse lonena za chimene iwo anali kunka kukachichita?—
Munthuyo anauika umodzi wa mikono yache kumbuyo kwa mapewa a Yesu. Iye anambiza Yesu pansi pa madzi kwa kamphindi chabe ndi kumbvuulanso iye. Iye anambatiza iye. Kodi nchifukwa ninji iye anachita chimenecho? Yesu anampempha munthuyo kuchita icho. Koma kodi chifukwa ninji? Kodi inu mukuchidziwa?—
Yesu anachichita icho kotero kuti Mulungu akadziwe kuti Yesu anafuna kumtumikira iye moyo wache wonse, inde, kosatha. Koma kodi Mulungu anamfuna Yesu kuti abizidwe pansi pa madzi motero?—Inde, iye anafuna. Kodi tikudziwa motani?—
Chifukwa chakuti pamene Yesu anabvuuka m’madzimo iye anawamva mau akuru ochokera kumwamba akuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga amene ndimkonda. Ine ndiri wokondwera kwambiri ndi iwe.’—Marko 1:9-11.
Kodi nchiani chimene Yesu anachichita pambuyo pa chimenechi?—Eya, iye anayamba kumayendayenda akumalankhula za Mulungu kwa munthu ali yense ankamvetsera. Iye anawauza iwo ponena za ufumu wa Mulungu. Iye anawauza iwo mmene iwo akadathera kukhala ndi moyo kosatha.
Amuna ndi akazi ena anakhulupilira zimene Mphunzitsi Wamkuruyo anawaphunzitsa iwo. Koma iwo anamva chisoni. Kodi inu mukuchidziwa chifukwa chache?—
Chifukwa chakuti iwo anaganizira zinthu zambiri zoipa zimene iwo anali atazichita. Iwo anadziwa kuti Mulungu sanali wokondweretsedwa ndi zinthu zimenezo. Iwo anadziwa kuti Baibulo linanena kuti zinthu zimenezo zinali zolakwa. Tsopano iwo anafuna kukhala ngati Yesu ndi kumkondweretsa Mulungu. Chotero, kodi inu mukuchidziwa chimene iwo anachichita?—
Iwo anapempha kuti abatizidwe monga momwe Yesu anabatizidwira. Iwo anafuna kumuuza Mulungu kuti iwo anamkonda iye ndi kuti iwo anafuna kumtumikira iye moyo wao wonse.
Ife tingathe kuchichita chinthu chimodzimodzicho lero lino. Ndithudi, inu mudakakulabe tsopano. Koma inu simudzauononga moyo wanu wonse mukumangokula, kodi sichocho?—Ndithudi ai. Tsiku lina inu mudzakhala mkulu. Kodi nchiani chimene inuyo mudzachichita pa nthawi imeneyo?—
Kodi inu mudzakhala ngati Yesu?—Kodi inu mudzachichita chimene amuna ndi akazi amene anamkhulupilira Yesu anachichita? Kodi inu mudzabatizidwa?—Ngati mutero, inu mudzakhala mukumamuuza Mulungu kuti inu mukumkonda iye. Inu mudzakhala mukumamuuza iye kuti inu mukufuna kumtumikira iye moyo wanu wonse. Ndikukhulupiliradi kuti inu muchita chimenecho. Ndipo Mulungu adzakhala wokondwera kwambiri ngati inu mutero.
Pamene munthu wakula, pali zinthu zambiri zimene iye angathe kuzichita. Anthu ena amene ali akulu amakhala limodzi ndi mabanja ao. Iwo amagwira nchito ndi kupeza ndarama, ndipo iwo amawagulira zinthu mabanja ao. Iwo amagula zobvala, chakudya, mipando, ngakhale magalimoto. Izi ziri zabwino kwambiri. Koma kodi imeneyi ndiyo njira ya kumuuzira Mulungu kuti iwo akumkonda iye? Kodi imeneyi ndiyo njira ya kumuuzira Mulungu kuti iwo akufuna kumtumikira iye moyo wao wonse?—
Ambiri a anthu amenewa samafunadi kumvetsera pamene munthu wina amayesayesa kulankhula nawo ponena za Baibulo. Iwo sangaliwerenge kumene Baibulo. Ena a iwo samalankhuladi kumene ponena za Mulungu kapena Mphunzitsi Wamkuruyo, ngakhale kwa ana ao. Ena a iwo sangamthokoze kumene Mulungu kaamba ka chakudya chimene iwo amadya, kapena kulankhula kwa iye m’pemphero usiku. Iwo samamkondadi Mulungu, ati?—Inu simukadafuna kukula ndi kukhala ngati iwo, kodi mukafuna kutero?—Ndi zachisoni chotani mmene zimenezo zikakhalira.
Mphunzitsi Wamkuruyo analankhula za Mulungu kwa anthu a mitundu yonse, kuphatikizapo ana ang’ono. Iye anakondwera ndi kulankhula za Mulungu ndi ponena za zinthu zabwino zimene Mulungu adzawachitira awo amene amamkonda iye. Iye anatanthauzadi chimenecho pamene iye anamuuza Mulungu kuti: ‘Atate, Ine ndikukukondani ndipo ndikufuna kutumikira inu kosatha.’ Phunzirani zonse zimene inu mungathe ponena za Mphunzitsi Wamkuruyo tsopano pamene inu mudakali ang’ono. Uloleni mtima wanu udzazidwe ndi chikondi kaamba ka Yehova Mulungu. Pamenepo inu, nanunso, mudzachitanthauzadi chimenecho pamene inu mumuuza Mulungu kuti: ‘Ine ndikukukondani ndipo ndikufuna kukutumikirani inu kosatha.’
(Malemba ena amene inu mungawawerenge amene amasonyeza mmene ife tingachisonyezere chikondi chathu kaamba ka Mulungu ndiwo: Mateyu 6:24-33; 24:14; 1 Yohane 2:15-17; 5:3.)