Mulungu Awononga Dziko Loipa
18 Ana a Adamu anachuluka. Iwo anakhalanso oipa kwambiri. Mulungu anaganizira za kuwawononga.—Genesis 6:1, 5, 7
19 Koma panali munthu wabwino wotchedwa Nowa.—Genesis 6:8, 9
Yehova Mulungu anamuuza kukhoma chibwato choti iye mwini ndi banja lake akapulumukiremo pamene anthu oipa akawonongedwa. Chibwato chimenechi chinapangidwa ngati chibokosi. Chinatchedwa chingalawa.—Genesis 6:13, 14
20 Iwo analowetsa nyama zambiri m’chingalawa.—Genesis 6:19-21
21 Yehova anachititsa mvula yochuluka kwambiri kugwa. Anthu onse oipa anafa. Awo amene anali m’chingalawa anapulumuka. Kodi mukudziŵa chifukwa chake?—Genesis 6:17; 7:11, 12, 21; 1 Petro 3:10-12