Mutu wa Buku Lino/Tsamba la Ofalitsa
Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
Chisungiko cha padziko lonse mu ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere” chiri chotsimikizirika kotheratu. Mulungu Wamphamvuyonse akutitsimikizira chimenechi mu ulosi wonena za kubadwa ndi ntchito ya “Kalonga wa Mtendere” pa Yesaya 9:6, 7: “Adzamutcha dzina lake . . . Kalonga wa Mtendere. Zakuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha . . . changu cha Yehova wamakamu chidzachita zimenezi.” Mmene oŵerenga bukhu lino angakonzekerere kuloŵa m’mwana alirenji wa ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere” kwalongosoledwa m’bukhu lino.
—Afalitsi.
Kugwidwa kwa mawu a m’Baibulo m’bukhu lino kwapangidwa kuchokera mu Revised Union Nyanja Version, ndi New World Translation of the Holy Scriptures, kope la 1984 (NW) akumakhala chidule chake.