Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 38
  • Kodi Yohane Anasoŵa Chikhulupiliro?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yohane Anasoŵa Chikhulupiliro?
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yohane Analibe Chikhulupiriro?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yohane Yemwe Anali M’ndende Ankafuna Kumva Kuchokera kwa Yesu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Yohane M’batizi Anali Ndani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 38

Mutu 38

Kodi Yohane Anasoŵa Chikhulupiliro?

YOHANE Mbatizi, amene wakhala m’ndende kwapafupifupi chaka tsopano, akulandira lipoti lonena za chiukiliro cha mwana wamwamuna wa mkazi wa masiye ku Naini. Koma Yohane akufuna kumva mwachindunji kuchokera kwa Yesu ponena za tanthauzo la zimenezi, chotero akutumiza aŵiri a ophunzira ake kukafufuza: “Kodi ndinu Wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?”

Limenelo lingawonekere kukhala funso lachilendo, makamaka popeza kuti Yohane anawona mzimu wa Mulungu ukutsikira pa Yesu ndi kumva liwu la Mulungu la chivomerezo pobatiza Yesu pafupifupi zaka ziŵiri zapitazo. Funso la Yohane lingachititse ena kugamula kuti chikhulupiliro chake chafooka. Koma zimenezi siziri choncho. Yesu sakanalankhula moyamikira kwambiri Yohane, zimene iye akuchita pachochitika ichi, ngati Yohane akanakhala atayamba kukayikira. Pamenepo, nchifukwa ninji, Yohane akufunsa funso limeneli?

Yohane angakhale akufuna kutsimikizira chabe kuchokera kwa Yesu kuti Iye ndiye Mesiya. Zimenezi zikakhala zolimbikitsa kwambiri kwa Yohane pamene akuvutika m’ndende. Koma mwachiwonekere funso la Yohane likuphatikizapo zambiri koposa zimenezo. Iye mwachiwonekere akufuna kudziŵa ngati pati padzakhale winanso wakudza, woloŵa mmalo, kunena kwake titero, amene adzatsiriza kukwaniritsidwa kwa zinthu zonse zimene zinanenedweratu zoti zidzachitidwe ndi Mesiya.

Malinga ndikunena kwa maulosi Abaibulo amene Yohane ali wozoloŵerana nawo, Wodzozedwa wa Mulungu ayenera kudzakhala mfumu, ndi wolanditsa. Komabe, Yohane adakali womangidwabe monga mkaidi, ngakhale miyezi yambiri pambuyo pa ubatizo wa Yesu. Chotero mwachiwonekere Yohane akufunsa Yesu kuti: ‘Kodi inu ndinudi woti adzakhazikitse Ufumu wa Mulungu mu ulamuliro wowoneka, kapena pali wina wosiyana nanu, woloŵa mmalo, amene tiyenera kuyembekezera kuti akwaniritse maulosi onse odabwitsa onena za ulemelero wa Mesiya?’

Mmalo mwa kuuza ophunzira a Yohane kuti, ‘Ndithudi ndine amene amene anali kudza!’ Yesu mu ola lomwelo akuchita chisonyezero chapadera mwa kuchiritsa anthu ambiri, akumawachiritsa matenda awo amitundumitundu ndi zowawa. Ndiyeno akuuza ophunzirawo kuti: “Mukani, muuze Yohane zimene mwaziwona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuwona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphaŵi ulalikidwa uthenga wabwino.”

Mwa mawu ena, funso la Yohane lingapereke lingaliro la chiyembekezo chakuti Yesu adzachita zowonjezereka koposa zimene akuchita ndipo mwinamwake adzamasula Yohane mwiniyo. Komabe, Yesu, akuuza Yohane kusayembekezera zozizwitsa zowonjezereka koposa zimene Yesu akuchita.

Pamene ophunzira a Yohane achoka, Yesu akutembenukira kumakamuwo ndi kuwauza kuti Yohane ndiye “mthenga” wa Yehova wonenedweratu m’Malaki 3:1 ndiponso ndiye mneneri Eliya wonenedweratuyo m’Malaki 4:5, 6. Motero iye akukweza Yohane kukhala wofanana ndi mneneri wina aliyense amene anakhalako iye asanakhale, akumafotokoza kuti: “Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa muufumu wakumwamba amkulira iye. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino ufumu wakumwamba uli wokangamizidwa.”

Panopo Yesu akusonyeza kuti Yohane sadzakhala mu Ufumu wakumwamba, popeza kuti wamng’ono kumeneko ndiye wamkulu koposa Yohane. Yohane anakonzekeretsa njira kaamba ka Yesu koma anafa Kristu asanasindikize pangano, kapena chigwirizano, ndi ophunzira ake, chakuti iwo akakhale olamulira limodzi naye mu Ufumu wake. Ndicho chifukwa chake Yesu akuti Yohane sadzakhala nawo mu Ufumu wakumwamba. Mmalomwake Yohane adzakhala nzika ya dziko lapansi ya Ufumu wa Mulungu. Luka 7:18-30; Mateyu 11:2-15.

▪ Kodi nchifukwa ninji Yohane akufunsa kuti kaya ngati Yesu ndiye Wakudzayo kapena ngati winawake ayenera kuyembekezeredwa?

▪ Kodi ndimaulosi otani amene Yesu akunena kuti Yohane akukwaniritsa?

▪ Kodi nchifukwa ninji Yohane Mbatizi sadzakhala ndi Yesu kumwamba?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena