Mutu 64
Phunziro la Kukhululukira
YESU mwachiwonekere adakali m’nyumba ku Kapernao limodzi ndi ophunzira ake. Iye wakhala akukambitsirana nawo mmene angasamalilire mavuto a pakati pa abale, chotero Petro akufunsa kuti: “Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye?” Popeza kuti aphunzitsi achipembedzo Chachiyuda amapereka lingaliro la kukhululukira kufikira katatu, mwinamwake Petro akulingalira kukhala kukoma mtima kwambiri kupereka lingaliro lakuti “kufikira kasanu ndi kaŵiri kodi?”
Koma lingaliro lonselo la kusunga cholembedwa choterocho nlolakwika. Yesu akuwongolera Petro kuti: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.” Iye akusonyeza kuti palibe malire amene ayenera kuikidwa pa chiŵerengero cha nthaŵi zimene Petro akhululukira mbale wake.
Kuti akhomereze pa ophunzirawo thayo lawo la kukhululukira, Yesu akuwauza fanizo lina. Nlonena za mfumu ina yofuna kutherana ngongole ndi akapolo ake. Kapolo wina akubweretsedwa kwa iye amene ali naye ngongole yaikulu ya madenari 60,000,000. Palibiretu njira yothekera imene angailipilire. Chotero, monga momwe Yesu akufotokozera, mfumuyo ikulamula kuti iyeyo ndi mkazi wake limodzi ndi ana ake agulitsidwe kuti athe kulipirirako.
Pakumva zimenezo kapoloyo akugwada pamapazi a mbuye wakeyo napempha kuti: “Bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.”
Atagwidwa ndi chisoni kaamba ka iye, mbuyeyo mwachifundo akuchotsera kapoloyo ngongole yake yaikuluyo. Koma mwamsanga atangochita zimenezo, Yesu akupitiriza kuti, kapoloyo akuchoka kukafunafuna kapolo mnzake yemwe anamkongola madenari 100. Munthuyu akugwira kapolo mnzake pakhosi nayamba kumkanyanga, akumati: “Bwezera chija unachikongola.”
Koma kapolo mnzakeyo alibe ndalama iriyonse. Motero akugwada pamapazi a kapolo womkongozayo, akumapempha kuti: “Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.” Mosiyana ndi mbuye wake, kapoloyo sali wachifundo, ndipo akuchititsa kapolo mnzakeyo kuponyedwa m’ndende.
Eya, Yesu akupitiriza kuti, akapolo ena amene anawona zimene zinachitika akupita kukanena kwa mbuyeyo. Iye mokwiya akuitana kapoloyo. “Kapolo woipa iwe,” iye akutero, “ndinakukhululukira iwe mangaŵa onse aja momwe muja unandipempha ine; kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?” Atakalipa ndi mkwiyo, mbuyeyo akupereka kapolo wopanda chifundoyo kwa osunga ndende kufikira atabweza ngongole yonse.
Ndiyeno Yesu akumaliza kuti: “Chomwechonso Atate wanga adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.”
Ndiphunziro labwino chotani nanga la kukhululukira! Poyerekeza ndi ngongole yaikulukulu ya uchimo imene Mulungu watikhululukira, tchimo lirilonse limene mbale wathu Wachikristu angatichitire liridi lochepa. Ndiponso, Yehova Mulungu watikhululukira kwanthaŵi zikwizikwi. Kaŵirikaŵiri, sitimazindikiradi machimo athu kwa iye. Chifukwa cha chimenecho, kodi sitingakhululukire mbale wathu nthaŵi zoŵerengeka, ngakhale ngati tiri ndi chifukwa choyenerera kudandaula? Kumbukirani, monga mmene Yesu anaphunzitsira mu Ulaliki wa pa Phiri, Mulungu ‘adzatikhululukira mangaŵa athu, monga ifenso takhululukira a mangaŵa athu.’ Mateyu 18:21-35; 6:12; Akolose 3:13.
▪ Kodi nchiyani chimene chikusonkhezera funso la Petro ponena za kukhululukira mbale wake, ndipo kodi nchifukwa ninji angalingalire lingaliro lake la kukhululukira wina kasanu ndi kaŵiri kukhala lokoma mtima?
▪ Kodi yankho la mfumu kupempho la kapolo wake lopempha chifundo likusiyana motani ndi yankho la kapoloyo kupempho la kapolo mnzake?
▪ Kodi timaphunziranji m’fanizo limeneli la Yesu?