Mutu 94
Kufunika kwa Pemphero ndi kwa Kudzichepetsa
POYAMBIRIRAPO pamene anali mu Yudeya, Yesu analankhula fanizo lonena za kufunika kwa kukhala wakhama m’pemphero. Tsopano, paulendo wake womaliza wa ku Yerusalemu, kachiŵirinso iye akugogomezera kufunika kwa kusaleka kupemphera. Mwinamwake Yesu ali m’Samariya kapena Galileya pamene akuuza ophunzira ake fanizo lowonjezereka ili:
“M’mudzi mwakuti munali woweruza wosawopa Mulungu, ndi wosasamala munthu. Ndipo m’mudzimo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiŵeruzire mlandu pa wotsutsana nane. Ndipo sanafuna nthaŵi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiwopa Mulungu kapena kusamala munthu; koma chifukwa cha kundivuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwake.”
Ndiyeno Yesu akugwiritsira ntchito nkhaniyo, akumati: “Tamverani chonena woweruza wosalungama. Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nawo mtima?”
Yesu sakutanthauza kuti apereke lingaliro lakuti Yehova Mulungu mwanjira iriyonse ngwofanana ndi woweruza wosalungamayo. Mmalomwake, ngakhale ngati woweruza wosalungamayo adzalabadira pempho losalekeza, sipayenera kukhala ndi chikayikiro chakuti Mulungu, amene ali ponse paŵiri wolungama ndi wabwino, adzayankha ngati anthu ake saleka kupe mphera. Chotero Yesu akupitirizabe kuti: “Ndinena ndi inu, [Mulungu] adzawachitira chilungamo posachedwa.”
Kaŵirikaŵiri chiweruzo cholungama sichiperekedwa kwa odzichepetsa ndi osauka, pamene kuli kwakuti anthu okhala ndi ulamuliro ndi olemera kaŵirikaŵiri amayanjidwa. Komabe, sikokha kuti Mulungu, adzatsimikizira kuti molungama oipa akulangidwa komanso adzatsimikizira kuti atumiki ake akuchitiridwa molungama mwa kuwapatsa moyo wosatha. Koma kodi ndianthu angati amene angakhulupilire mwamphamvu kuti Mulungu adzachititsa chiweruzo cholungama kuchitidwa mofulumira?
Posonya makamaka kuchikhulupiliro chogwirizanitsidwa ndi mphamvu ya pemphero, Yesu akufunsa kuti: “Koma Mwana wa munthu pakudza iye, adzapeza chikhulupiliro padziko lapansi kodi?” Ngakhale kuti funsolo likusiyidwa liri losayankhidwa, lingaliro lake lingakhale liri lakuti chikhulupiliro choterocho sichikakhala chofala pamene Kristu adza mumphamvu ya Ufumu wake.
Pakati pa awo amene akumvetsera Yesu pali ena amene akulingalira kukhala odzitsimikizira m’chikhulupiliro chawo. Iwo amadzidalira kuti ali olungama, ndipo amanyoza ena. Ena mwa ophunzira a Yesu angaphatikizidwenso m’kagulu kameneka. Chotero iye akulunjikitsa fanizo lotsatirapoli kwa otero:
“Anthu aŵiri anakwera kumka kukachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu; ndisala chakudya kaŵiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndiri nazo.”
Afarisi ngodziŵika ndi kudziwonetsera kwawo kukhala olungama poyera kuti achititse chidwi ena. Masiku awo ozoloŵereka a kusala chakudya kofunikira ndiwo Lolemba ndi Lachinayi, ndipo iwo mwachinyengo amalipira chakhumi ngakhale cha timasamba tonunkhira tam’munda. Miyezi ingapo yapitayo, kunyoza kwawo anthu wamba kunawonekera mkati mwa Phwando la Misasa pamene iwo anati: “Khamu ili losadziŵa Chilamulo, [ndiko kuti, matanthauziridwe a Afarisi operekedwa pa ilo] likhala lotembereredwa.”
Popitiriza fanizo lake, Yesu akuwauza za munthu ‘wotembereredwa’ wotero kuti: “Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso ake kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.” Chifukwa chakuti wamsonkhoyo anavomereza modzichepetsa machimo ake, Yesu akunena kuti: “Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, osati uja ayi; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.”
Motero kachiŵirinso Yesu akugogomezera kufunika kwa kudzichepetsa. Pokhala oleredwera m’chitaganya chimene Afarisi odzilungamitsa ali achisonkhezero kwambiri ndipo malo audindo ndi ntchito zimagogomezeredwa nthaŵi zonse, kuli kosadabwitsa kuti ngakhale ophunzira a Yesu akuyambukiridwa. Komabe, ndiphunziro labwino kwambiri chotani nanga la kudzichepetsa limene Yesu akuphunzitsa! Luka 18:1-14; Yohane 7:49.
▪ Kodi nchifukwa ninji woweruza wosalungama akuvomereza pempho la mkazi wamasiye, ndipo kodi ndiphunziro lanji limene likuphunzitsidwa ndi fanizo la Yesu?
▪ Kodi Yesu adzafunafuna chikhulupiliro chotani pamene afika?
▪ Kodi nkwayani kumene Yesu akulunjikitsa fanizo lake lonena za Mfarisi ndi wamsonkho?
▪ Kodi ndikaimidwe kamaganizo kotani ka Afarisi kamene kayenera kupeŵedwa?