Mutu 98
Ophunzira Akangana Pamene Imfa ya Yesu Iyandikira
YESU ndi ophunzira ake ali pafupi ndi Mtsinje wa Yordano, umene akudutsa kuchokera m’chigawo cha Pereya kuloŵa m’Yudeya. Anthu ena ambiri akuyenda nawo limodzi kumka ku Paskha wa 33 C.E., amene wangotsala kokha sabata limodzi kapena chapompo.
Yesu ali patsogolo pa ophunzira ake, ndipo iwo ali odabwa ndi chitsimikiziro chake champhamvu. Kumbukirani kuti masabata oŵerengeka apapitawo pamene Lazaro anamwalira ndipo Yesu anali pafupi kunyamuka mu Pereya kumka mu Yudeya, Tomasi analimbikitsa ena kuti: “Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.” Kumbukiraninso kuti Yesu ataukitsa Lazaro, Sanhedrin inalinganiza chiwembu cha kupha Yesu. Mposadabwitsa kuti mantha amenewo agwira ophunzirawo pamene iwo tsopano akuloŵanso m’Yudeya.
Powakonzekeretsa zimene ziri mtsogolo, Yesu akutengera 12 amenewo pambali mwamtseri ndi kuwauza kuti: “Tawonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa akulu ansembe ndi alembi; ndipo adzamnyoza iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.”
Imeneyi ndinthaŵi yachitatu m’miyezi yaposachedwapa pamene Yesu wauza ophunzira ake za imfa ndi chiukiliro chake. Ndipo ngakhale kuti akumumvetsera, iwo akulephera kuzindikira. Mwinamwake chiri chifukwa chakuti iwo amakhulupilira kuti ufumu wa Israyeli udzabwezeretsedwa padziko lapansi, ndipo iwo akuyang’anira mtsogolo kukulandira ulemerero ndi ulemu muufumu wa Kristu wapadziko lapansi.
Pakati pa aulendo omka ku Paskhayo pali Salome, amayi a atumwiwo Yakobo ndi Yohane. Yesu anatchula amuna ameneŵa kuti “Ana a Bingu,” mosakayikira chifukwa cha kaimidwe kawo ka maganizo kotukutira. Kwanthaŵi yakutiyakuti aŵiri ameneŵa akhala ndi lingaliro lodzikweza la kukhala otchuka mu Ufumu wa Kristu, ndipo auza zikhumbo zawozo kwa amawo. Amayiwo tsopano akufika kwa Yesu mmalo mwawo, nagwada pamaso pake, ndi kumpempha kukomeredwa mtima.
“Ufuna chiyani?” Yesu akufunsa motero.
Iye akuyankha kuti: “Lamulirani kuti ana anga aŵiri ameneŵa adzakhale, wina kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, muufumu wanu.”
Pozindikira magwero a pempholo, Yesu akunena kwa Yakobo ndi Yohane: “Inu simudziŵa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere ine?”
“Ife tikhoza,” iwo akuyankha motero. Ngakhale kuti Yesu wangowauza kumene kuti iye akuyang’anizana ndi chizunzo chowopsa ndipo potsirizira pake kuphedwa, iwo mwachiwonekere sakuzindikira kuti izi ndizo zimenezi akutanthauza mwa mawu akutiwo “chikho” chimene ati amwere.
Komabe, Yesu akuwauza kuti: “Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.”
M’nthaŵi yokwanira atumwi ena khumi adziŵa zimene Yakobo ndi Yohane apempha, ndipo iwo ngokwiya. Mwinamwake Yakobo ndi Yohane anali onkitsa mumkangano woyambilira wa pakati pa atumwiwo wonena zakuti wamkulu ndani. Pempho lawo lapanthaŵi ino likuvumbula kuti sanagwiritsire ntchito uphungu umene Yesu anapereka pankhaniyi. Momvetsa chisoni, chikhumbo chawo cha kudzikweza chidakali champhamvube.
Chotero kuthetsa mkangano watsopanowu ndi mkhalidwe woipa umene wapanga, Yesu akuitana 12 amenewo pamodzi. Powadzudzula mwachikondi, iye akuti: “Mudziŵa kuti mafumu a anthu amadziyesera okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.”
Yesu wapereka chitsanzo chimene iwo ayenera kutsanzira, pamene akufotokoza kuti: “Monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” Sikokha kuti Yesu anatumikira ena koma kuti iye adzachita motero kufikira kumlingo wa kufera anthu! Ophunzirawo afunikira kaimidwe ka maganizo konga ka Kristu kamodzimodziko ka kukhumba kutumikira mmalo mwa kutumikiridwa ndi ka kukhala wamg’ono mmalo mwa kukhala pamalo okwezeka. Mateyu 20:17-28; Marko 3:17; 9:33-37; 10:32-45; Luka 18:31-34; Yohane 11:16.
▪ Kodi nchifukwa ninji mantha akugwira ophunzira?
▪ Kodi Yesu akukonzekeretsa motani ophunzira ake zimene ziri mtsogolo?
▪ Kodi ndipempho lotani limene likupangidwa kwa Yesu, ndipo kodi atumwi enawo akuyambukiridwa motani?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akuthetsera vuto lapakati pa atumwi?