Mutu 132
Kudzanja Lamanja la Mulungu
KUTSANULIRIDWA kwa mzimu woyera pa Pentekoste kuli umboni wakuti Yesu wafika kumwamba. Masomphenya operekedwa mwamsanga pambuyo pake kwa wophunzirayo Stefano akutsimikiziranso kuti Iye wafika kumeneko. Pamene Stefano akuponyedwa miyala kaamba ka kuchitira umboni kwake kokhulupirika, iye akufuula kuti: “Tawonani, ndipenya m’mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu alikuimirira pa dzanja la manja la Mulungu.”
Pamene ali kudzanja lamanja la Mulungu, Yesu akuyembezera lamulolo kuchokera kwa Atate wake: “Chitani ufumu pakati pa adani anu.” Koma pakali pano, kufikira pamene achitapo kanthu motsutsana ndi adani ake, kodi Yesu akuchitanji? Iye akulamulira, kapena kuchita ufumu, pa ophunzira ake odzozedwa, kuwatsogolera m’ntchito yawo yolalikira ndi kuwakonzekeretsa kukhala, mafumu anzake mu Ufumu wa Atate wake mwa chiukiriro.
Mwachitsanzo, Yesu akusankha Saulo (amene pambuyo pake akudziŵika bwino ndi dzina lake Lachiromalo, Paulo) kupititsa patsogolo ntchito yakupanga ophunzira m’maiko ena. Saulo ali wachangu ku Chilamulo cha Mulungu, komabe akutsogoleredwa molakwa ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda. Monga chotulukapo, sikokha kuti Saulo akuvomereza kuphedwa mwambanda kwa Stefano koma kuti akupita ku Damasiko mwachilolezo cha mkulu wansembe Kayafa kukagwira ndi kubweretsa ku Yerusalemu amuna ndi akazi otsatira Yesu amene iye akawapeza kumeneko. Komabe, pamene Saulo ali panjira, kuunika kwakukulu kukuŵala mwadzidzidzi momzinga ndipo akugwera pansi.
“Saulo, Saulo, undilondalonderanji?” liwu lochokera kumagwero osawoneka likufunsa motero. “Ndinu yani Mbuye?” Saulo akufunsa.
“Ndine Yesu amene umlondalonda,” yankho likudza.
Saulo, amene wachititsidwa khungu ndi kuunika kozizwitsako, akuuzidwa ndi Yesu kuloŵa m’Damasiko ndi kuyembekezera malangizo. Pamenepo Yesu akuwonekera m’masomphenya kwa Hananiya, mmodzi wa ophunzira ake. Ponena za Saulo, Yesu akuuza Hananiya kuti: “Iye ndiye chotengera changa chosankhika, cha kunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli.”
Ndithudi, mochirikizidwa ndi Yesu, Saulo (wodziŵika tsopano monga Paulo) ndi alaliki ena ali ndi chipambano chachikulu m’ntchito yawo ya kulalikira ndi kuphunzitsa. Kunena zowona, pafupifupi zaka 25 pambuyo pa kuwonekera kwa Yesu kwa iye panjira yomka ku Damasiko, Paulo akulemba kuti “uthenga wabwino,” walalikidwa ‘m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.’
Patapita zaka zambiri, Yesu akupereka mpambo wa masomphenya kwa mtumwi wake wokondedwa, Yohane. Kudzera mwa masomphenya ameneŵa amene Yohane akusimba m’bukhu la Baibulo la Chivumbulutso, iye, m’chenicheni, akukhala ndi moyo kuwona Yesu akubwera m’mphamvu ya Ufumu. Yohane akunena kuti ‘mogwidwa ndi mzimu’ anatengeredwa kunthaŵi yamtsogolo ku “tsiku la Ambuye.” Kodi “tsiku” limeneli nchiyani?
Kupenda kosamalitsa kwa maulosi Abaibulo, kuphatikizapo ulosi wa Yesu mwiniyo wonena za masiku otsiriza, kumavumbula kuti “tsiku la Ambuye” linayamba m’chaka chosaiŵalika m’mbiri cha 1914, inde, mkati mwa mbadwo unowo! Chotero munali mu 1914 pamene Yesu anabweranso mosawoneka, popanda dzoma lapoyera la kumchingamira ndipo atumiki ake okhulupirika okha akumazindikira kubweranso kwake. M’chakacho Yehova analamula Yesu kuchita ufumu pakati pa adani ake!
Pomvera lamulo la Atate wake, Yesu anayeretsa miyamba kuchotsa Satana ndi ziŵanda zake, kuwaponyera pansi kudziko lapansi. Atawona zimenezi zikuchitika m’masomphenya ameneŵa, Yohane akumva mawu ochokera kumwamba akumalengeza kuti: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake!” Inde, mu 1914 Kristu anayamba kulamulira monga Mfumu!
Ndimbiri yabwino chotani nanga imeneyi kwa olambira Yehova kumwamba! Iwo akufulumizidwa kuti: “Kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo.” Koma kodi ndimkhalidwe wotani umene uli kwa awo okhala padziko lapansi? “Tsoka mtunda ndi nyanja,” liwu lakumwambalo likupitirizabe kuti, “chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”
Tikukhala mkati mwa nyengo ya kanthaŵiko tsopano. Tsopano lino anthu akulekanitsidwira kaya kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu kapena kuwonongedwa. Chowonadi nchakuti, mtsogolo mwanu mukutsimikiziridwa tsopano mwanjira imene mumalabadirira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu imene ikulalikidwa padziko lonse lapansi motsogozedwa ndi Kristu.
Pamene kulekanitsidwa kwa anthu kumalizidwa, Yesu Kristu adzatumikira monga Woimira wa Mulungu kuchotsa padziko lapansi dongosolo lonse la zinthu la Satana ndi onse amene amalichirikiza. Yesu adzatsiriza kuchotsa kwa kuipa konse kumeneku m’nkhondo yotchedwa Harmagedo kapena Armagedo, m’Baibulo. Pambuyo pake, Yesu, Munthu wamkulu woposa onse m’chilengedwe wachiŵiri kwa Yehova Mulungu mwiniyo, adzagwira Satana ndi ziŵanda zake ndi kuwamanga zaka chikwi ku “phompho,” ndiko kuti, mkhalidwe wa kusagwira ntchito wonga imfa. Machitidwe 7:55-60; 8:1-3; 9:1-19; 16:6-10; Salmo 110:1, 2; Ahebri 10:12, 13; 1 Petro 3:22; Luka 22:28-30; Akolose 1:13, 23; Chivumbulutso 1:1, 10; 12:7-12; 16:14-16; 20:1-3; Mateyu 24:14; 25:31-33.
▪ Yesu atakwera kumwamba, kodi iye akukhala kuti, ndipo kodi akuyembekezeranji?
▪ Kodi Yesu akulamulira ayani atakwera kumwamba, ndipo kodi ulamuliro wake ukuwonekera motani?
▪ Kodi ndiliti pamene “tsiku la Ambuye” linayamba, ndipo nchiyani chinachitika pakuyamba kwake?
▪ Kodi ndintchito yakulekanitsa yotani imene ikuchitidwa lerolino imene imayambukira aliyense wa ife payekha, ndipo ndipamaziko otani pa amene kulekanitsidwa kukuchitidwa?
▪ Ntchito yakulekanitsa itamalizidwa, kodi ndizochitika zotani zimene zidzatsatira?