Chikuto Chakumbuyo
TSIKU LA YEHOVA . . . imeneyi ndi nkhani yaikulu yomwe yatchulidwa mobwerezabwereza m’mabuku 12 omaliza a Malemba Achiheberi. Anthu ambiri sakuwadziwa bwino mabuku aulosi amenewa. Koma m’mabukuwa mungapezemo mfundo zothandiza zimene mungazigwiritse ntchito pa moyo wanu watsiku ndi tsiku. Komanso kuphunzira mabukuwa kungakuthandizeni kukonzekera tsiku lalikulu la Yehova.