MUTU 24
Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza
Yehova anauza Mose kuti: ‘Bwera kuphiri kuno. Ndilemba malamulo anga pamiyala n’kukupatsa.’ Mose anapita kuphiriko ndipo anakhalako masiku 40. Ali komweko, Yehova analemba Malamulo 10 pamiyala iwiri n’kumupatsa.
Patapita nthawi, Aisiraeli anaganiza kuti Mose wawathawa. Choncho anauza Aroni kuti: ‘Tikufuna mtsogoleri wina. Tipangire mulungu.’ Aroni anawauza kuti: ‘Ndipatseni golide wanu.’ Ndiyeno anasungunula golideyo n’kupanga fano la mwana wa ng’ombe. Zitatero, Aisiraeliwo anati: ‘Uyu ndi Mulungu amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.’ Iwo anayamba kulambira fano la mwana wa ng’ombelo ndipo anachita mwambo wokondwerera fanolo. Kodi ukuganiza kuti zimenezi zinali zabwino? Ayi, chifukwa anthuwo anali atalonjeza kuti azilambira Yehova yekha. Koma zimene anachitazi zinali zosemphana ndi zimene analonjeza.
Yehova anaona zimene zinkachitikazi ndipo anauza Mose kuti: ‘Pita ukaone zimene anthu aja akuchita. Asiya kundimvera ndipo akulambira mulungu wabodza.’ Mose anatsika m’phirimo atanyamula miyala iwiri ija.
Atayandikira msasa uja anamva anthu akuimba. Kenako anawaona akuvina komanso kugwadira mwana wa ng’ombe uja. Mose anakwiya kwambiri. Anaponya pansi miyala iwiri ija moti inasweka. Nthawi yomweyo anawotcha fanolo n’kuliperapera. Kenako anafunsa Aroni kuti: ‘Kodi anthuwa akuchitira chiyani kuti uwamvere n’kuchita zinthu zoipa chonchi?’ Aroni anayankha kuti: ‘Pepani musandikwiyire. Mukudziwa bwino mmene anthuwa alili. Iwo amafuna mulungu ndiye ndinangotenga golide n’kumuponya pamoto ndipo panatuluka mwana wang’ombeyu.’ Komatu Aroni sankayenera kuchita zimenezi. Mose anapitanso kuphiri kuja n’kukapempha Yehova kuti akhululukire anthuwo.
Yehova anakhululukira anthu onse amene analapa n’kuyambiranso kumumvera. Kodi ukuona chifukwa chake zinali zofunika kuti Aisiraeli azimvera zonse zimene Mose ankawauza?
“Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako, chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu opusa. Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.”—Mlaliki 5:4