Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb tsamba 106-107
  • Mawu Oyamba Gawo 8

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu Oyamba Gawo 8
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Solomo Anali Mfumu Yanzeru
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Ino Ndi Nthawi Yofunika Kuchitapo Kanthu Mwachangu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Solomo Ndi Chitsanzo Chabwino Kapena Choipa?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mudzakhulupirika Monga Eliya?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb tsamba 106-107
Mfumu Solomo inapeza mayi weniweni wa mwana

Mawu Oyamba Gawo 8

Yehova anadalitsa Solomo pomupatsa nzeru komanso mwayi woti adzamange kachisi. Koma patapita nthawi Solomo anasiya kulambira Yehova. Ngati ndinu kholo, fotokozerani mwana wanu mmene anthu olambira milungu yabodza anachititsira kuti Solomo asiye kulambira Yehova. Ufumu wa Isiraeli unagawanika ndipo mafumu oipa anachititsa kuti anthu asiye kulambira Mulungu n’kumalambira mafano. Pa nthawi imeneyo, atumiki ambiri a Yehova ankazunzidwa kapenanso kuphedwa kumene. Mfumukazi Yezebeli inachititsa kuti anthu a mu ufumu wakumpoto azilambira kwambiri mafano. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri kwa Aisiraeli. Komabe panali anthu ena amene ankatumikira Yehova mokhulupirika. Ena mwa anthuwa anali Mfumu Yehosafati komanso mneneri Eliya.

ZIMENE TIPHUNZIRE M’CHIGAWOCHI

  • Muzitumikira Yehova mokhulupirika ngakhale anthu a m’banja lanu kapena anzanu atasiya kumutumikira

  • Mukasiya kutumikira Yehova, palibe chimene chingayende. Koma mukamamutumikirabe adzakudalitsani

  • Nthawi zambiri munthu akamaona kuti akusowa mtengo wogwira, Yehova amamuthandiza m’njira yoti samayembekezera

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena