NYIMBO 4
“Yehova Ndi M’busa Wanga”
Losindikizidwa
1. Yehova ndi M’busa wanga
Sindidzasowa kanthu.
Amadziwa zofuna zanga
Zomwe ndi zofunika.
Amanditsogolelanso
M’malo otetezeka.
Mwachikondi chakedi chosatha
Wandipatsa mtendere.
Mwachikondi chake chosatha
Wandipatsa mtendere.
2. Zochita zanu n’zabwino,
Zonse n’zachilungamo.
Zochita zanga nthawi zonse
Zikulemekezeni.
Pamene ndikuvutika
Mumandithandizadi.
Sindidzaopatu chilichonse
Chifukwa muli nane.
Sindidzaopa chilichonse
Chifukwa muli nane.
3. M’lungu ndinu M’busa wanga,
Ndidzakutsatirani.
Mumandilimbikitsa ndithu.
Mumandipatsa zonse.
Poti ndinudi wamphamvu
Ndimakudalirani.
Kukoma mtima kwanu kosatha
Muzindisonyezabe.
Kukoma mtimatu kosatha
Muzindisonyezabe.
(Onaninso Sal. 28:9; 80:1.)