NYIMBO 21
Muziika Ufumu Pamalo Oyamba
Losindikizidwa
1. Chinthu chapadera chomwe
Tikuchidikirira
Ndi Ufumu wa Mulungu
Womwe ukonze zonse.
(KOLASI)
Muike Ufumu wake
Poyamba nthawi zonse
Ndipo muzimutamanda
Ndi kumutumikira.
2. Musade nkhawa za mawa,
Za chakudya ndi madzi.
Mulungu adzatipatsa
Zofunikira zonse.
(KOLASI)
Muike Ufumu wake
Poyamba nthawi zonse
Ndipo muzimutamanda
Ndi kumutumikira.
3. Choncho muzilalikira.
Muzithandiza anthu
Kuti adalire M’lungu
Ndi Ufumu wakenso.
(KOLASI)
Muike Ufumu wake
Poyamba nthawi zonse
Ndipo muzimutamanda
Ndi kumutumikira.
(Onaninso Sal. 27:14; Mat. 6:34; 10:11, 13; 1 Pet. 1:21.)