Wamitala Ndiponso Mmapondera Apeza Chowonadi
Mwamuna wa ku Afirika wotchedwa Isake, limodzi ndi amuna ena, anachoka ku Tchalitchi cha Apositoliki cha mmudzi mwake chifukwa sichinali kuchita zomwe chinaphunzitsa. Pambuyo pake onse, kuphatikizapo akazi awo, anakhala Mboni za Yehova—kupatulapo Isake. Iwo analingalira za kumuchezera ndi kumuwuza kuti apeza chowonadi. Isake, panthawiyo, anali mapondera wopambana ndipo anali ndi akazi ambiri. Pambuyo pa kuphunzira kabukhu ka Sangalalani ndi Moyo Pa Dziko Lapansi Kosatha! lochita ndi njira yake ya moyo, Isake anasiya umapondera wake, womwe umamubweretsera ndalama zambiri, ndipo akazi ake kusiyapo mkazi wamkulu. lye analembetsa ukwati wake kwa mkazi wake wamkulu, yemwe anali ndi zaka 63 (iye anali 68). lye akuti akumva kukhala “wachimwemwe kwambiri ndi womasuka sawopanso mizimu.”