“Lemekezani Dzina la Yehova”
Pa September 2, 1986, Ripabuliki la German Democratic (East Germany) linatulutsa ndandanda ya masitampu osonyeza ndalama za mu mbiri za German. Ndalama yoyambirira mu ndandandayo yasonyezedwa pansipa. Ndalama yosonyezedwayo iri ndi deti la 1633. Komabe, chochititsa chidwi chapadera chiri zilembo zinayi zosangalatsa za Chihebri zosonyezedwa molembedwa pa ndalamayo. Kodi nchiyani chimene zimatanthauza? Briefmarkenwelt, magazini ya Chigerman pa kusonkhanitsa masitampu, ikupereka kulongosola uku: “Angelo awiri, olenjekeka pamwamba pa mzinda, akunyamula pakati pawo dzina lakuti Yehova.”
Mkati mwa zaka za zana la 16 ndi 17, chinali chofala kwambiri kupanga ndalama zoterozo mu Europe. Encyclopedia yakale ya Chigerman yokhala ndi deti la 1838 ikuchitira ndemanga: “Liwu lakuti ndalama za Yehova limaphatikiza ndalama zonse ndi mamedulo omwe amasonyeza liwu lakuti יהוה Yehova, likuwala, kaya lokha kapena limodzi ndi liwu lakuti Yesu, . . . kawirikawiri ndi mawu ofala mu kulozera ku chimenecho; popeza ichi poyambirira chikupezeka pa ma Taler ambiri [ndalama za siliva zoperekedwa ndi maboma osiyanasiyana a Chigerman pakati pa zaka za zana la 15 ndi 19], iwo aikidwa mu gulu limodzi pansipa dzina lakuti ndalama za siliva za Yehova.”
Mwachidziwikire, anthu ambiriwo ogwiritsira ntchito masitampu amenewo sakudziwa kuti malemba a Chihebri amaimira dzina la Mulungu. Koma Mboni za Yehova ziri zachimwemwe kuloza ku chidziwitso chimenechi pa sitampu ndi kulongosola tanthauzo ndi kufunika kwa dzina la Yehova. Chotero, kuchokera ku malo osayembekezereka iwo athandizidwa “kulemekeza dzina la Yehova.”—Masalmo 135:1.