‘Ana Amalikonda Ilo’
Mamiliyoni a mabanja asangalala ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Nkhani zake za Baibulo 116 zimapereka kwa wowerenga lingaliro la chimene Baibulo limakamba. Kumayambiriro kwa chaka chino munthu wa ku Western Australia anapereka chitsanzo cha mmene bukhuli liriri lokhutiritsa, akumalongosola kuti:
“Ine ndimagwira ntchito yauphunzitsi ndipo ndimafunafuna kusonkhezera ana omwe ali pansi pa chisamaliro changa kupereka ntchito yawo yonse ya ku sukulu kwa Mulungu ndi Yesu, monga mmene ndimachitira mofananamo mu ntchito yanga kaamba ka ana. Ndinachipanga icho kukhala nsonga ya ntchito kuwerenga ku kalasi ‘Bukhu la Nkhani za Baibulo’ lanu lomwe ndinagula kuchokera kwa mmodzi wa Mboni zoitanira zanu. Ana amalikonda bukhulo, nkhani zimene ziri mmenemo, ndi kundipempha ine kaamba ka zowonjezereka pamene ndiika bukhulo pansi.”
Kodi pali ana amene mumawadziwa omwe angasangalalenso ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo? Mungalandire kope mwakudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka. Bukhulo liri ndi masamba 256, ukulu wofanana ndi tsamba la magaziniyi ilo liri ndi zithunzithunzi zazikulu zoposa 125, zambiri za izo ziri mu mtundu wokongola.
Chonde nditumizireni, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekeramo K20. 00.