“Nsanja ya Olonda” pa Kaseti Iyamikiridwa
Anthu owonjezerekawonjezereka akhala akulongosola chiyamikiro choterocho. Wachichepere wochokera ku Alberta, Canada, akulemba kuti:
“Ndine mtsikana wa zaka 17 zakubadwa yemwe amavutika ndi matenda a kulankhula, vuto la kuphunzira. Nthaŵi zonse ndinakhala ndi vuto la kukhala wokhoza kumvetsetsa zochepera kuchokera ku zomwe ndiŵerenga. Komabe, ngati wina wake atenga nthaŵi kuŵerenga chidziŵitsocho kwa ine, ndingamvetsetse icho nthaŵi yomweyo.
“M’nthaŵi yapita, nthaŵi zonse chinakhala chokwiyitsa, ngakhale chokhumudwitsa, kuŵerenga Nsanja ya Olonda. Tsopano ichi chasintha mozizwitsa. Ndangomaliza kaseti yokwaniritsa ya kope la January 1. Mawu sangalongosole mmene chiriri chosangalatsa kumvetsetsa chomwe ndaŵerenga, kuchokera ku chikuto kufika ku chikuto! Ndiri wothokoza kwambiri, woyamikira, ndi wa chiyamiko kaamba ka makonzedwe atsopano amenewa.”
Kodi inu mungakondwere kukhala ndi winawake akuŵerenga kope iriyonse ya Nsanja ya Olonda kwa inu kaamba ka chaka chotsatirachi? Chabwino, chotero, dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka, limodzi ndi chopereka choyenerera, ndi kulandira Nsanja ya Olonda pa matepi a kaseti. Kujambulidwa kwa kope iriyonse pa kaseti imodzi kudzatumizidwa kwa inu, makaseti 2 pa mwezi, 24 kaamba ka kulembetsa kwa chaka. Chopereka chiri kokha K360. Kwa anthu otsimikiziridwa monga akhungu kapena mwakuthupi osakhoza kuŵerenga zinthu zoŵerenga za nthaŵi zonse, kulembetsa kwa chaka chimodzi kuli kokha K120.
Chonde tumizani kulembetsa kwa chaka chimodzi kaamba ka matepi a kaseti a Nsanja ya Olonda. Chongani bokosi loyenerera, ndi kutumiza chopereka choyenerera. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)
□ Chingelezi, chaka chimodzi. Ndatsekeramo K360 (Zambia).
□ Chingelezi, chaka chimodzi. Ndatsekeramo K120 (Zambia), limodzinso ndi chitsimikiziro cha kupunduka kwanga (monga chomwe chaperekedwa ndi magulu kaamba ka akhungu, adokotala, kapena akatswiri a kukonzanso).