Iye Anangofunikira Kudziŵa
Mtsikana wa zaka 15 zakubadwa wa ku Mobile, Alabama, akulemba kuti: “Pamene munatulutsa bukhu la Revelation—Its Grand Climax At Hand! ndinadziŵa kuti ndidzaliŵerenga ilo posachedwa kapena pambuyo pake.
“Usiku wina pamene sindinali kugona bwino, ndinanyamula bukhulo ndi kungoyang’ana pa zithunzithunzi. Pa masamba 75, 78, ndi 86, ndinapeza zithunzithunzi zimene zinandichititsa chidwi. Sindinadziŵe chimene izo zinatanthauza, ndipo ndinangofunikira kudziŵa. Sindikanatha bwino lomwe kuyambira pakati chifukwa mwakutero panalibe chirichonse chimene chikapanga nzeru. Chotero usiku womwewo ndinaŵerenga mutu woyamba.
“Usiku wotsatira ndinaŵerenga mutu wotsatira ndikupeza kuti sindanangofuna kuliika ilo pansi. Chotero ndinapitiriza ndi kuŵerenganso wotsatira.
“Iri ndi limodzi la mabukhu ochititsa chidwi omwe ndaŵerenga chikhalire! Tsopano ndiri ndi chizolowezi chokhazikika cha kuŵerenga mosachepera pa mutu umodzi usiku uliwonse. Nthaŵi zina ndinakhala maso kufikira ora loyamba m’maŵa ndikungoŵerenga! . . . Ndikukhumba kuti achichepere onse akaŵerenga bukha limeneli.”
Timadzimva otsimikizirika kuti nanunso mudzasangalatsidwa ndi zinthu zimene mudzaphunzira mu Revelation—Its Grand Climax At Hand! Bukhu limeneli la chikuto cholimba liri la ukulu wa masamba wofanana ndi magazini ino. Ilo limapereka kulingaliridwa kwa versi ndi versi kwa bukhu la Baibulo lonse la Chibvumbulutso, kupereka kalongosoledwe komvekera bwino ka masomphenya ake ambiri ndi zizindikiro. Tumizani kaamba ka bukhulo lero. Kokha K30, titalipiriratu positi.
Chonde tumizani bukhu la masamba 320 Revelation—Its Grand Climax At Hand! Ndatsekeramo K30 (Zambia).