Nchiyani Chimene Baibulo Limanena Ponena za Kuchotsa Mimba?
Chimenecho nchomwe okwatirana aŵiri mu Argentina anafunsa mkazi wowachezera iwo, popeza iwo anadziŵa kuti mkaziyo anali wozoloŵerana bwino lomwe ndi Baibulo. Okwatiranawo anafuna kudziŵa ngati Mulungu analingalira kuchotsa mimba kukhala koyenera. Mkaziyo anali atakhala ndi pakati kwa miyezi iŵiri ndipo anali kukonzekera za kuchotsa mimba, ngakhale kuti mwamuna wake sanavomereze.
Mkazi wochezera okwatiranayo anatulutsa kope la bukhu la Reasoning From the Scriptures ndi kutsegula pa tsamba 25. Iye anaŵerenga tanthauzo la kuchotsa mimba ndipo kenaka anaŵerengetsa okwatiranawo malemba ondandalitsidwa m’chofalitsidwacho, kusonyeza mmene Mulungu amawonera mwana wosabadwa. Miyezi isanu ndi iŵiri pambuyo pake khandalo linabadwa. M’nthaŵi imeneyi, makolo onyadirawo anali atakhala ophunzira a Baibulo.
Inu mungalandire kope laumwini la bukhu la Baibulo laphindu limeneli lachikhuto cholimba limene lidzapereka mayankho ku mazana angapo a mafunso a panthaŵi yake.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikhuto cholimba, lokhoza kunyamulidwa m’manja lamasamba 448 lakuti Reasoning From the Scriptures. Ndatsekeramo K15, Zambia.