Chipwirikiti Sichingaletse Mbiri Yabwino
TSIKU lina February yapita, dongosolo latsopano la chuma cha Venezuela loyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali linalengezedwa. Mitengo inkakwezedwa kuposa ndi 100 peresenti pa zakudya za nthaŵi zonse monga ngati mkaka, ufa wa tirigu, ndi mkate. Mitengo ya mafuta a galimoto ikakwera ndi 90 peresenti. Mitengo ya maulendo inalamulidwa kukwezedwa ndi 30 peresenti. Dzikolo linadodometsedwa. Mwadzidzidzi, Lolemba, February 27, anthu anayamba kupanga chipwirikiti dziko lonselo.
M’mawa wotsatira, zinthu zinali zitafika pachimake pa kuwonongeka ndi kufunkha. Kulira kwa mfuti kunali kumveka m’malo ambiri. Achichepere ndi achikulire anawukira m’makwalala a mzindawo, akumasiya kumbuyo nkukuluzi wa chiwonongeko chomwe chinafanana ndi bwalo lankhondo losakazidwa ndi nkhondo.
Masana amenewo prezidenti wadzikolo analengeza lamulo loikidwa m’nthaŵi ya ngozi ndi kuleketsa kugwira ntchito kwa mpambo wa malamulo nthaŵi zonse kwa masiku khumi. Kuletsa kuyenda kunayambitsidwa kaamba ka maola kuchokera pa 6:00 p.m. ndi 6:00 a.m. Tsiku lotsatira, nduna ya zachitetezo inalengeza kuti kuletsa kuyendako kukapitirira kufikira pa nthaŵi ina. Gulu lankhondo linagwiritsira ntchito ulamuliro wake kuyang’anira makwalala, kuloŵa m’nyumba popanda chilolezo, ndiponso kuimika ndi kufufuza anthu. “Mazana aŵiri afa ndipo chikwi chimodzi avulazidwa mkati mwa chisokonezo cha masiku atatu,” inasimba tero nyuzipepala ina.
Kodi ndimotani mmene mipingo ya Mboni za Yehova inali kuchitira mkati mwa chipoloŵe chimenechi? Abalewo anapatsidwa uphungu wakuti: Khalani ochenjera ndi kupeŵa malo amavuto. Sinthani nthaŵi ya misonkhano kotero kuti mugwirizane ndi kuletsa kuyenda, ndipo peŵani kulalikira m’magulu aakulu. Komabe, kulalikira kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kunapita patsogolo.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Chifukwa chakuti mwamuna wosakhulupirira wa mkazi wina Wachikristu anali wodera nkhaŵa ponena za ubwino wake ngati akanapita kunja kukalalikira, iye analetsa mkaziyo kuchoka. “Simukumvetsetsa kuti ndiri ndi thayo loti ndilikwaniritse,” mkaziyo anamuuza iye. “Chotero bwerani tsopano! Ndidzaphunzira Baibulo ndi inu!”
Imeneyi inali nthaŵi yoyamba m’zaka 22 za mkaziyo monga Mboni kuti mwamunayo anasonyeza kufunitsitsa kwa kuphunzira Baibulo. Chikhalirechobe mwamunayo anapereka chenjezo lakuti: “Chabwino, kokha ngati ulonjeza kuti sudzapita panja. Koma osandifunsa mafunso, dzingondiŵerengera.” Mosasamala kanthu za izo, mlongoyo anaphunzira naye kwa ola limodzi ndi theka. “Linali phunziro lachitsanzo, labwino koposa limene sindinakhalepo nalo ndi kalelonse m’zaka zanga 22 m’chowonadi,” iye anatero, pamene misozi inadzaza m’maso mwake.
M’chochitika china, mpainiya wokhazikika ankasesa kanjira ka kunja kwa nyumba yake pamene anafikiridwa ndi mkazi yemwe mwa nthaŵi zonse sakanamvetsera kwa Mboni pamene zikachezera nyumba yake. “Sindinakuwoneni Mboninu kwa kanthaŵi,” anatero mkaziyo. “Musandiuze kuti simudzalalikira konse!”
Mlongoyo analongosola kuti iwo aleka kulalikira kunyumba ndi nyumba kokha mkati mwa chipwirikiticho. “Koma tsiku lidzafika pamene sitidzalalikiranso kwa anthu, ndipo chidzatanthauza mapeto a dziko,” anatero mlongoyo. “Muyenera kugwiritsira ntchito mwaŵi ulipowu ndi kulandira phunziro la Baibulo m’nyumba mwanu.”
“Kodi ndi liti pamene tingapange makonzedwe?” mkaziyo anafunsa mofulumira. Makonzedwe anapangidwa pa nthaŵi yomweyo a kuyamba phunziro la Baibulo lapanyumba.
Moyamikirika, kusakhazikikako kunaleka, kulola mkhalidwe wa dzikolo kubwerera mwakale. Komabe, m’mikhalidwe yowopsya yoteroyo, chiri chitonthozo kudziŵa kuti posachedwapa dziko latsopano la mtendere ndi chisungiko lidzabwera. Mawu a Mulungu akulonjeza kuti: “Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Ndipo kokha ngati Mulungu alola, Mboni za Yehova zidzapitiriza kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.
[Zithunzi patsamba 31]
Kusakhazikika sikunaimitse olengeza a Ufumu
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi chotengedwa ndi Publicaciones Capriles, Caracas, Venezuela