Chinachake Chabwinopo Kuposa Wailesi Yakanema
Mayi wina wa ku Indianapolis, Indiana, U.S.A., akulemba kuti wangowodera mwana wake wamwamuna wazaka zinayi zakubadwa, seti yachiŵiri ya makaseti tepi (Achingelezi) a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Iye akuulula kuti: “Nthaŵi zambiri pamene ife, atate wake ndi ine, tikupenyerera wailesi yakanema m’chipinda chochezeramo, iye adzakhala m’khichini akumaseŵera ndi kumvetsera ku nkhani za Baibulo. Zimativutitsa kwambiri chakuti timazimitsa wailesi yakanema.“
Iye akumaliza kuti: “Tiri otsimikiza kuti matepi a Nkhani za Baibulo amthandiza kukhala kamnyamata kabata ndi kachimwemwe. . . . Tikuthokozani kwabasi.”
Kumvetsera ku makaseti a nkhani 116 za mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kuli njira yodabwitsa kwa achichepere yophunzirira Baibulo. Mwana wachichepere angakumbukire kuposa zimene mukulingalira ngati ali nacho chikondwerero. Mabanja ambiri apeza Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ndi kujambulidwa kwa bukhulo pa makaseti tepi, kukhala zofunikira kudzutsa chikondwererocho. Mungalandire makaseti tepiwo kapena volyumu ya Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kapena zonse ziŵiri, mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Chongani chimodzi kapena ziŵiri zotsatirazi, ndi kutumiza chopereka cholondola:
□Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, alubamu ya mtundu wa brown vinyl ndi makaseti tepi anayi (Achingelezi) a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Ndatsekeramo K160 (Zambia). (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)
□Chonde tumizani bukhu la zithunzithunzi lamasamba 256 la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, limene ndatsekeramo K60 (Zambia).