Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 4/1 tsamba 21-22
  • Kutumikira Katswiri Wojambula Kuposa Onse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutumikira Katswiri Wojambula Kuposa Onse
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Luso Nchiyani?
    Galamukani!—1995
  • Waluso wonyalanyazidwa koposa m’Nthaŵi Yathu
    Galamukani!—1995
  • Ndinasankha Ntchito Yabwino
    Galamukani!—2010
  • Chinthu Chokhalitsa Kuposa Luso la Zosemasema ndi Zoumbaumba
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 4/1 tsamba 21-22

Kutumikira Katswiri Wojambula Kuposa Onse

MONGA msungwana wachichepere wa zaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa, ndinayamba kudzifunsa kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji ndidzafunikira kufa? Kodi kuli kotheka kupewa imfa?’ Ndinali nditauzibwa kuti Mulungu amatenga anthu abwino chifukwa chakuti amawafuna kuti akakhale naye kumwamba. Ndikali kukumbukirabe mmodzi wa amkalasi mwanga akudzuma kuti: “Kuli bwino kwambiri kukhala munthu woipa chifukwa chakuti abwino amayamba kufa!”

Ndinakonda zojambula, chotero ndinayamba kuphunzira luso la kujambula. Kusukulu, ndinalibe mpata wa kulingalira nkhani za chipembedzo, ndiponso ndinalibe nthawi ya kuzikondwerera. Kwenikweni, ndinalikuuza mabwenzi anga kuti munthu kukhala wopembedza, afunikira mlingo wotsika wanzeru. Pamene ndinamaliza maphunziro anga aukatswiri wojambula, ndinapatsidwa malo antchito auphunzitsi wa zojambula m’sukulu yapamwamba.

Ndinakonda ntchito yanga ndipo ndinali wokondwereranso Chitaliyana ndi mabuku achilendo, nyimbo zophatikizapo zitsanzo ndi ndakatulo, ndi sewero. Chinthu chokha cha chipembedzo chimene ndinaphunzira nthaŵi imeneyo chinali nkhani zojambula zithunzi za ojambula mnyengo zosiyanasiyana. Ndiyeno ndinaphunzira chimene chimatanthauza kukhala paphata lachisamaliro, chimene kuwonetsera ntchito ya munthuwe kunali, chimene kulemekezedwa kwambiri kunatanthauza, kutamandidwa, ndi kuyamikiridwa monga katswiri wojambula.

Nthaŵiyo, kujambula zithunzi kunatanthauza zambiri kwa ine, chifukwa chakuti munali m’ntchitoyo mmene ndinapeza chifukwa chachikulu chimene ndinaliri wamoyo. Komatu mafunso amene ndidawafunsa pamene ndinali wa zaka zisanu ndi ziŵiri analimobe mmaganizo mwanga. Ndinafunafuna mwakhama kanthu kena kozama kwambiri, kanthu kena kamene ndinali wosakhozabe kufotokoza. Ndinali woŵerenga wakhama ndipo ndinafunsa anthanthi kaamba ka malongosoledwe. Mulimonse mmene zinaliri, ndinafuna yankho lachindunji pa zikaikiro zanga.

Ndinali chikhalirebe ndi chisokonezo chimenechi pamene ndinakwatiridwa. Pambuyo pa kubadwa kwa mwana wanga wamkazi, kufunafuna kwanga chowonadi kunakula kwambiri. Ndinayesa kukupeza mwa kujambula ndi utoto, kulemba ndakatulo, kumvetsera nyimbo, ndi kuŵerenga mabuku. Nthaŵi iriyonse nditapita kukonsati ndikumvetsera mawu oyambirira a nyimbo, mwachibadwa maganizo anga anakumbukira Mulungu, Namalenga amene sindinadziŵe, ndipo ndinam’yamika. Kaŵirikaŵiri nthaŵi imeneyo, ndinatamanda Mulungu kaamba ka zinthu zokongola zimene ndinakhumbira​—khanda langa logonalo, mawonekedwe a zithunzithunzi zojambulidwa ndi utoto. “Nzomvetsa chisoni chotani nanga,” ndinkadzuma motero, “kuti ukatswiri wojambula ndi utoto, umene unakakhala ndi zinthu zochuluka kwambiri zokongola, kuti uyenera kugwiritsidwa ntchito kwambiri chotere kulongosola imfa mmalo mwa moyo!” Zina za ndakatulo zabwino kwambiri ndi nyimbo za mkanema ziri kaya nyimbo zodzetsa chiyembekezo kapena zosonyeza malingaliro achisoni kapena masoka; zithunzi zina zabwino kwambiri zojambulidwa mwaluso zimatamanda imfa mmalo mwa kutamanda moyo ndi kukongola kwake. Chifukwa ninji?

Malingaliro otsutsana amenewa anandilefula kwambiri, ndipo pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukhala wamphwayi. Munali mumkhalidwewo mmene Mboni za Yehova zinafika pakhomo panga. Pamene ndinazimvetsera, kunali ngati kuti zinali kulankhula nane m’chinenero chatsopano. Lonjezo la Mulungu la kupanga dziko lapansi paradaiso linamvekera kukhala nyimbo yokondweretsa kumakutu anga. Ndinayamba kuŵerenga Baibulo. Potsirizira pake ndinapezamo mayankho a mafunso amene sindinaleke kufunsa kuyambira pamene ndinali wa zaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa. Mulungu samafuna kuti anthu afe koma akulinganiza kudalitsa atumiki ake okhulupirika mwa kuwapatsa moyo wosatha padziko lapansi!

Munali mu 1973. Chaka chotsatira ndinapanga kudzipereka kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa. Sikunali kosavuta kuti mkhalidwe wanga wansontho ndi mtima wapachala ziloŵedwe mmalo ndi mzimu wa chikondi chaubale chowona, kudzidalira kwanga kuloŵedwe mmalo ndi kupanda dyera, ndipo kudzisangulutsa kuloŵedwe mmalo ndi mzimu wa kudzimana! Ndinafunikira kudzikana. Mboni za Yehova zandithandiza kwambiri, monga yachitira misonkhano yochitidwira pa Nyumba Yaufumu.

Katswiri Wojambula Wamkulu wathetsa zikaikiro ndi zothetsa nzeru zanga. Ndimamuyamikira chotani nanga! Ndicho chifukwa chake, chiyambire September 1984, ndakhala mu utumiki wa upainiya wokhazikika, ndikumathera maola 90 mwezi uliwonse kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.

Kutumikira Katswiri Wojambula Wamkulu ndi Mlengi, Yehova, limodzi ndi banja langa kulidi kokhutiritsa maganizo. Tikuyembekezera mwaphamphu nthaŵi pamene adzajambula chithunzi chochititsa nthumanzi kuposa zonse; pamene potsirizira pake adzachotsa dongosolo lakale, ndi loipa limene ladetsa ndi kukuta dziko lapansi iri. Imfa sidzakhalakonso, ndipo pamenepo zithunzithunzi za utoto zidzasonyeza moyo wokha. Pamenepo, kukongola kokha kudzasonyezedwa, chifukwa chakuti kupyolera mwa dongosolo latsopano lolungama la Mulungu, chisoni ndi ululu zidzakhala zitachotsedwa kosatha.​—Yoperekedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena