Kodi Mukalandira Mlendo?
Mmodzi wa Mboni za Yehova angafune kukuchezerani ndi kukuthandizani kuwonjezera chidziŵitso chanu chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi zifuno zake monga momwe zalembedwera m’Baibulo. Tiri achidaliro kuti chidziŵitso chimenechi chidzakuthandizani, popeza chidzapereka mayankho odalirika amavuto amene tonsefe tikuyang’anizana nawo lerolino. Mboni za Yehova zimapereka chilangizo cha m’Baibulo kwa aliyense payekha ndi kugulu popanda malipiro.
Motero ngati mungafune kuchezeredwa ndi munthu woyeneretsedwa panyumba panu, kapena pamalo ena oyenerera, tidzakhala osangalala kupanga makonzedwe. Mudzathandizidwa kupeza osati kokha mayankho a mafunso anu a Baibulo komanso mayankho a mavuto amene angathetsedwe mwakugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo. Kuti mupindule inu eni ndi utumiki umenewu, tangolembani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
(Kunja kwa U.S.A., lemberani nthambi ya Watch Tower ya kumaloko kaamba ka chidziŵitso. Wonani tsamba 2.)