Iye Anapeza Katrakiti Panjanji
MUNALI m’chaka cha 1921. M’mapiri a Transvaal, dera la South Africa, gulu la amuna okonza njanji ankagwira ntchito panjanji yasitima. Kapitawo wa gululo, wolankhula Chiafrikaner wotchedwa Christiaan Venter, anawona kachidutswa kapepala kosomekedwa kunsi kwa njanji. Iko kanali katrakiti kofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society.
Pamene analamulira amuna ake kuima, Christiaan anakaŵerenga ndi chikondwerero chachikulu. Iye anathamangira kukakomana ndi mkamwini wake, Abraham Celliers, namufotokozera mokondwera kuti: “Abraham, lero ndachipeza chowonadi!”
Mwamsanga pambuyo pake, iwo analembera afalitsi a katrakitiko kuti amve zambiri. Powayankha, nthambi ya ku South Africa ya Watch Tower Society inaŵatumizira mabuku owonjezereka a Baibulo. Amuna aŵiriwa anaŵaphunzirira pamodzi pa nthaŵi ya kupuma kwawo ndiusiku kwambiri. Mofulumira anayamba kugawana chowonadicho ndi mabwenzi ndi alendo.
Pomalizira pake, onse aŵiri Christiaan ndi Abraham anakhala Mboni zobatizidwa za Yehova. Monga chotulukapo cha changu chawo ndi kukhulupirika, anthu ambiri a ku South Africa anathandizidwa kudziŵa chowonadi. Kuwonjezera apa, mbadwa zawo zoposa zana limodzi ziri Mboni za Yehova zokangalika lerolino! Mmodzi wa iwo akutumikira pamalikulu a Mboni za Yehova m’Brooklyn, New York, ndipo wina ali pa ofesi ya Watch Tower Society mu South Africa.
Lerolino, zaka 70 pambuyo pake, matrakiti a Baibulo akupitirizabe kuchita mbali yaikulu m’kufalitsa uthenga Waufumu.