“Kugwirizananso kwa Banja Lapadziko Lonse”
Tangoganizirani za kukhala ndi mabwenzi ndi banja m’maiko 212. Kodi nchosatheka? Ayi, nchothekera. Mboni za Yehova nzaubale Wachikristu wa padziko lonse. Izo zimalambira Yehova Mulungu ndipo zimagaŵana mbiri yabwino ya Ufumu wolamulidwa ndi Kristu Yesu ndi anthu onse amene adzamvetsera.
Ŵerengani malipoti osangalatsa onena za ntchito yawo mu 1991 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. M’ŵerengi wina analemba kuti: “Ndimayembekezera kukhala nayo Yearbook chaka chirichonse. Kumafanana ndikuwona kugwirizanso kwa banja lapadziko lonse pamene ndiŵerenga zokumana nazo zambiri zosangalatsa ndi ndemanga zochokera kwa mabwenzi.”
1991 Yearbook ikusonyeza ntchito za Mboni za Yehova mu Hawaii, Sweden, ndi Thailand. Kuwonjezerapo, iyo ikupereka mbiri yatsopano ya ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita padziko lonse. Ngati mungakonde kulandira bukhu lamasamba 256 limeneli, chonde dzazani ndikutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira 1991 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kumaloko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)