Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 3/1 tsamba 32
  • Kodi Mawonekedwe Ngofunika Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mawonekedwe Ngofunika Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1991
w91 3/1 tsamba 32

Kodi Mawonekedwe Ngofunika Motani?

“Ndinakwiitsidwa ndi mawonekedwe anga,” akulemba motero wachichepere wa ku Beaver Falls, Pennsylvania, U.S.A. “Ndinadzilingalira kukhala wonyansa ndi wosakongola.” Iye akulongosola kuti: “Sindinkadya kanthu kwa masiku angapo, ndipo ndinkataya mapaundi ena akulemera, koma ndinkamva njala kwambiri chifukwa cha kusadya kwakuti ndinkagwidiza zakudya tsiku lotsatira ndikupezanso kulemera kwanga.”

Pambuyo pake, pamsonkhano Wachikristu, iye anati: “Ndinadziyang’ana m’kalirole ndikunena kwa bwenzi langa kuti, ‘Ndikuwoneka moipa kwambiri!’

“Bwenzi langa lapamtima limeneli linandifunsa ngati ndinaŵerenga chigawo chakuti ‘A Look at How You Look’ m’bukhu lakuti Questions Young People Ask​—Answers That Work. Ndinati ayi. Iye anati kwa ine, ‘Wokondedwa, ukapita kunyumba usiku walero uyenera kuliŵerenga.’ Ndipo ndinachitadi zimenezo.

“Ndinadzimva ngati kuti ndinkaŵerenga nkhani ya moyo wanga. Kenaka ndinapeza funso limene linandipangitsa kulingalira, ‘Kodi ndani amene amapititsa patsogolo lingaliro lakuti ufunikira kukhala ndi mawonekedwe akutiakuti ngati uti ukondedwe, kukhala wachipambano, kapena wachimwemwe?’”

Wachichepereyu anati, yankho la funsoli linapangitsa masinthidwe aakulu m’moyo wake. Iye anamaliza kuti: “Kupyolera mwa malingaliro othandiza a m’bukhu la Young People Ask, ndinawona kufunika kwakulungamitsa zinthu zanga zofunika choyamba.”

Achichepere ali ndi zipsinjo zambiri lerolino. Amafunikira thandizo kuti azilake. Questions Young People Ask​—Answers That Work limapereka thandizo limeneli. Mungalandire kope la bukhu la zithunzithunzi zokongola limeneli mwakudzaza ndikutumiza kapepalaka.

Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 320 lakuti Questions Young People Ask​—Answers That Work. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena