Ndale Zadziko—Kodi Ziri Mbali ya Ntchito ya Uthenga Wabwino?
MALINGA ndikunena kwa Joachim Meisner, akibishopu wa ku Cologne ndi yemwe kale adali mtsogoleri wachipembedzo wotchuka wa Jeremani Wakum’mawa, “kuli chipanduko kutcha ndale zadziko kukhala zoipa, kuti ndintchito imene munthu amadetsa nayo manja ake.” Pofunsidwa mu 1989, iye anati: “Ndale zadziko ndichenicheni cha moyo ndipo nchifukwa chake izo ziri mbali ya ntchito yathu ya uthenga wabwino. Tiyenera kuchifikira chitokosocho. Mwanjira yotsimikiza, tiyenera kuloŵerera chiungwe chirichonse chandale zadziko, kuyambira kwa mayuniyoni a antchito ndi zigwirizano mpaka ku zipani zandale zadziko, tikumakhazikitsa m’magulu ameneŵa ndi m’zipanizo maziko a khalidwe Lachikristu limene anthu angaligwiritsire ntchito kupititsa patsogolo ndale zadziko za m’Jeremani ndi Yuropu.”
Mawu ogwidwa otsatirapoŵa kuchokera mu Frankfurter Allgemeine Zeitung, nyuzipepala yotchuka koposa Yachijeremani, amasonyeza kuti atsogoleri achipembedzo ambiri a ku Yuropu—ponse paŵiri Akatolika ndi Aprotestanti—amavomereza lingaliro la Meisner.
“Masiku asanu ndi limodzi okha pambuyo pa kusankhidwa kwake [October 1978], iye [papa] analengeza kuti monga munthu wa ku Yuropu Yakum’mawa sanafune kulandilira udindowo mu Yuropu. . . . Ena anakutenga kukhala ulaliki, koma iko kunali programu yandale zadziko.”—November 1989.
“M’malo ena [m’Chekosolovakiya] tchalitchi chinapata ulemu wapamwamba chifukwa chokhala patsogolo m’chipwirikiticho. Ophunzira pa semina ya ansembe m’Litomĕr̆ice, tauni ya kumpoto kwa Bohemia yokhala ndi tchalitchi cha cathedral, . . . anatsogolera chiukiro chopanda chiwawa m’November yapita.”—March 1990.
“Pemphero la mlungu ndi mlungu la mtendere m’Tchalitchi cha Nikolai [Chachiprotestanti], chimene kwa zaka khumi sichinazindikiridwe kwenikweni, mwadzidzidzi chinakhala chizindikiro cha chipwirikiti chaka chino, cha kuukira kopanda chiwawa mu GDR [German Democratic Republic]. . . . Atsogoleri achipembedzo osaŵerengeka ndi anthu wamba am’mipingo anakhala ndi phande m’ziwonetsero zochitidwa pambuyo pake.”—December 1989.
Pamene ankafunsidwa, Akibishopu Meisner ananenanso kuti: “Sitingadikirire andale zadziko Achikristu kugwa kuchokera kumwamba. . . . Sindimatopa kulimbikitsa Akristu achichepere . . . kuti adziloŵetse m’moyo wandale zadziko [kapena] . . . kumauza nzika zikulu kuti: Simuyenera kulola masankho kukupitani popanda kudziloŵetsamo.”
Moyenerera, ziŵalo 19 za Volkskammer (nyumba yamalamulo) ya ku Jeremani Yakum’mawa zosankhidwa paudindo m’March 1990 zinali atsogoleri achipembedzo. Chipembedzo chinaimiridwanso bwino lomwe m’bungwe la nduna zolamulira. Ponena za mmodzi wa atsogoleri achipembedzo ake atatu, Nduna ya Chitetezo Rainer Eppelmann, wolumbira kukana nkhondo, nyuzipepala ya Nassauer Tageblatt inasimba kuti: “Ambiri amamulingalira kukhala mmodzi wa atsogoleri a kuukira kwamtendere.”
Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu, zofika chiŵerengero cha zikwi mazana ambiri, zikusangalala ndi ufulu wachipembedzo wowonjezereka umene zirinawo tsopano. Komabe izo sizikuugwiritsira ntchito kudziloŵetsa m’mikangano yandale zadziko kapena yamayanjano. Mogwirizana ndi ntchito ya uthenga wabwino yotchulidwa pa Mateyu 24:14, izo zikutsatira chitsanzo cha Yesu chakukana ndale zadziko za anthu, zimakhala zachangu nthaŵi zonse kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokha cha anthu. Atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko—kaya Kum’mawa kwa Yuropu kapena kwina kulikonse—akakhala anzeru kuchita mofananamo.—Yohane 6:15; 17:16; 18:36; Yakobo 4:4.