Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 4/15 tsamba 28
  • Kodi Mumakumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yesu Amatchedwanso Mikayeli, Mkulu wa Angelo?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Mikaeli Mngelo Wamkulu Ndani?
    Galamukani!—2002
  • Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 4/15 tsamba 28

Kodi Mumakumbukira?

Kodi mwapeza makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda kukhala aphindu logwira ntchito? Pamenepa bwanji osayesa chikumbukiro chanu ndi zotsatirazi?

◻ Kodi ndimfundo zotani zomwe zimatsutsa kupatulikitsa malo olingaliridwa kukhala obadwira Yesu?

Baibulo silimatchula malo enieni obadwira Yesu. Zolembedwa za Mauthenga Abwino za Mateyu ndi Luka zimatchula kokha zinthu zofunika. (Mateyu 2:1, 5; Luka 2:4-7) Kuŵerenga Yohane 7:40-42 kumasonyeza kuti anthu mwachisawawa sankadziŵa kumene anabadwira, ena akumaganiza kuti iye anabadwira m’Galileya. Ndiponso, m’nthaŵi yamoyo wa Yesu wapadziko lapansi, iye sanabukitse tsatanetsatane wa kubadwa kwake.​—12/15, tsamba 5.

◻ Kodi Mkristu angasunge motani chimwemwe chake poyang’anizana ndi ziyeso za matenda akuthupi, kuchita tondovi, ndi mavuto achuma?

Mawu a Mulungu amapereka chitonthozo chofunikira ndi chitsogozo. Mwakuŵerenga kapena kumvetsera kuŵerengedwa kwa masalmo, chitsitsimulo choposa chofunikiracho chingapezedwe. Davide anatilangiza kuti: “Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza; Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” Iye anatitsimikizanso kuti Yehova alidi “Wakumva pemphero.” (Salmo 55:22; 65:2) Gulu la Yehova, kupyolera m’zofalitsidwa zake ndi akulu a mumpingo, nlokonzeka nthaŵi zonse kutithandiza kulimbana ndi mavuto athu.​—1/1, masamba 14-15.

◻ Kodi nchiyani chimene Yesu anatanthauza pamene ankapita kukapachikidwa, pomwe iye anati: ‘Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?’ (Luka 23:31)

Yesu anali kusonya ku mtengo wa mtundu Wachiyuda. Chifukwa cha kukhalapo kwa Yesu ndi kukhalapo kwa Ayuda otsalira amene anamkhulupirira, mtunduwo unali udakali ndi uwisi wamoyo. Komabe, pamene onseŵa anachotsedwa pakati pa mtunduwo, mtengo wakufa mwauzimu wokha ndiwo ukatsala, gulu louma la mtunduwo.​—1/15, tsamba 9.

◻ Kodi “oyera mtima,” otchulidwa pa Mateyu 5:8, (NW) “adzawona Mulungu” motani?

Iwo ‘amawona Mulungu’ pamene amamuwona iye akuchita mokomera osunga umphumphu. (Yerekezerani ndi Eksodo 33:20; Yobu 19:26; 42:5.) Komabe, liwu Lachigiriki lomasuliridwa ‘kuwona’ pa Mateyu 5:8 limatanthauzanso “kuwona ndi maganizo, kuzindikira, kudziŵa.” Popeza kuti Yesu anawunikira mwangwiro umunthu wa Mulungu, kukhala ndi chidziŵitso cha umunthu umenewo kunatheketsa “oyera mtima” ‘kuwona Mulungu.’ (Yohane 14:7-9)​—1/15, tsamba 16.

◻ Kodi nchifukwa ninji tikutsimikizira kuti Yesu ndiye Mikayeli mngelo wamkulu?

Mawu a Mulungu amangotchula kokha mngelo wamkulu mmodzi, ndipo amalankhula za mngeloyo pamene asonya kwa Ambuye Yesu woukitsidwayo kumati: ‘Pakuti Ambuye adzatsika kumwamba mwiniyekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu.’ (1 Atesalonika 4:16) Pa Yuda 9 timapeza kuti dzina la mngelo wamkuluyu ndi Mikayeli.​—2/1, tsamba 17.

◻ Kodi ndimbali zinayi ziti mmene tingachitire ulemu anthu ena?

Tiyenera kuchitira ulemu olamulira andale zadziko, otilemba ntchito, ziŵalo za banja, ndi omwe ali mumpingo.​—2/1, masamba 20-2.

◻ Imfa ya Yesu isanachitike, kodi nchitsanzo chabwino chotani chimene iye anakhazikitsira awo okhala ndi makolo okalamba?

Pamene Yesu adaali wolenjekeka pamtengo wozunzirapo m’nsautso, iye anapereka chisamaliro kuubwino wakuthupi ndi wauzimu wa amayi ŵake mwa kuŵaikiza ku chisamaliro cha mtumwi wake wokondedwa Yohane. (Yohane 19:25-27)​—2/15, tsamba 8.

◻ Kodi nchifukwa ninji Yesu anayenera kuvutika?

Mavuto a Yesu anatumikira kuthetsa nkhani ya umphumphu wa atumiki a Mulungu. Ndiponso anamkonzekeretsa kaamba ka udindo wake monga Mkulu Wansembe wachifundo wa anthu. (Ahebri 4:15)​—2/15, masamba 14-15.

◻ Kodi ndinkhani zofunika zotani zimene zinadzutsidwa ndi chipanduko m’Edene?

Kodi munthu angakhoze kudzilamulira mwachipambano popanda Mulungu? Kodi kuli kolungama kwa Mulungu kufuna chigonjero ku ulamuliro wake? Kuwonjezerapo, kodi anthu ena alionse akakhoza kusankha mopanda dyera kutumikira Mulungu modzifunira?​—3/1, tsamba 6.

◻ Kodi nchifukwa ninji ena anadya molakwika ziphiphiritso za Chikumbutso?

Ena opanda uchikulire angakhale alibe kuzindikira kolinganizika kwa zifuno za Mulungu. Iwo angakhale osazindikira kuti kudzozedwa “sikufuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu.” (Aroma 9:16) Sichiri kwa munthuyo kusankha kuti angakonde kutengedwera m’pangano latsopano ndikukhala woloŵa nyumba mnzake wa Kristu. Chosankha cha Yehova ndicho chiri nkanthu, ndipo mzimu wake umachitira umboni chosankhacho. (Aroma 8:16; 1 Akorinto 12:18)​—3/15, tsamba 21.

◻ Kodi “chinenero choyera” chofotokozedwa pa Zefaniya 3:9, (NW) nchiyani?

Ndicho kumvetsetsa kwabwino kwa chowonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake.​—4/1, masamba 21-2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena