Kodi Mungakonde Kuchezeredwa?
Mmodzi wa Mboni za Yehova angafune kukuchezerani ndi kukuthandizani kuwonjezera chidziŵitso chanu chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi zifuno zake, monga momwe zalembedwera m’Baibulo. Tiri achidaliro kuti chidziŵitso chimenechi chidzakuthandizani, popeza kuti chidzapereka mayankho odalirika a mavuto amene tonsefe tikuyang’anizana nawo lerolino. Mboni za Yehova zimapereka chilangizo cha m’Baibulo kwa aliyense payekha ndi kugulu popanda malipiro.
Chotero ngati mungafune kuchezeredwa ndi munthu woyeneretsedwa panyumba panu, kapena pamalo ena oyenerera, tidzakhala osangalala kukupangirani makonzedwe. Mudzathandizidwa kupeza osati kokha mayankho a mafunso anu a Baibulo komanso mayankho a mavuto alerolino amene angathetsedwe mwakugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Kuti mupindule inueni ndi utumiki umenewu, tangolembani mawu ofunidwa pansipa ndi kutumiza ku keyala iri pakapepalaka.
Ndingakonde kudziŵa zowonjezereka ponena za Baibulo. Chonde linganizani kuti wina adzandichezere.