Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
Kuthira mwazi kwakhala kukutamandidwa kwambiri kukhala njira yachisungiko, yopulumutsa moyo. Koma Dr. Alan A. Waldman akulongosola kuti: “Kulingalira kwabata kosatsutsika kwa chisungiko cha zinthu zopangidwa ndi mwazi kunasinthidwa modabwitsa pamene AIDS yogwirizana ndi kuthira mwazi inazindikiridwa.”
Komabe AIDS sindiyo ngozi yokha yomwe ilipo. “Zochitika zina zingapo zachititsa lingaliro lakuti pali ngozi zosadziŵika ndi zosalamulirika m’kugwiritsira ntchito mwazi woperekedwa,” Dr. Waldman akusonyeza motero. “Tsopano, ngakhale zinthu zomwe zinalingaliridwa kuti zinathetsedwa—mwachitsanzo, kukhutiritsa kwa kupima kaamba ka tizilombo tonyamula hepatitis B—kwakaikiridwa.”—Diagnostics & Clinical Testing, July 1989.
Ndithudi, mwazi ndichinthu chowopsa. Panthaŵi imodzimodziyo, mwazi ngwofunika kupulumutsa moyo. Kodi mwazi ungapulumutse motani moyo wanu? Mudzapindula mwakusanthula funsoli m’brosha yamasamba 32 yakuti How Can Blood Save Your Life?
Ngati mungakonde kulandira kope, chonde lembani ndikutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira brosha yamasamba 32 ya How Can Blood Save Your Life? (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)