Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/1 tsamba 32
  • Galamukani! Ithandiza Kulandira Mphotho mu Italiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Galamukani! Ithandiza Kulandira Mphotho mu Italiya
  • Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/1 tsamba 32

Galamukani! Ithandiza Kulandira Mphotho mu Italiya

Chaka chatha msungwana wasukulu wazaka khumi mu Italiya analemba nkhani pamutu wakuti “Ngati Dziko Lapansi Likanalankhula.” Nkhani ya mutuwo inafotokozedwa monga kukambitsirana pakati pa dziko lapansi ndi khanda lomwe linafunsa dziko lapansi chifukwa chake linali kulira. Msungwana wasukuluyo akufotokoza kuti:

“Dziko lapansi linayankha kuti linaipitsidwa ndi chifunga chomwe chinapangitsa kutentha kopambanitsa. Dziko lapansi linapitiriza kulankhula ndi khandalo ndikunena kuti posachedwapa zinthu zidzasintha ndipo mtsogolo mwake mukakhala mwabwinopo, mosasamala kanthu za munthu. Chiyembekezo cha dziko lapansi chinali mwa Mulungu Wamphamvuyonse, Mlengi wake, yemwe sanalenge dziko lapansi mwachabe koma kuti anthu akhalemo.​—Yesaya 45:18.”

Msungwana wasukuluyo ananenanso kuti: “Ndinatenga chidziŵitso changa m’magazini a Awake! a July 22, 1989; September 8, 1989; ndi September 22, 1989. Chifukwa cha magaziniŵa, nkhani yanga inalandira mphotho yoyamba. Mphotho yachiŵiri inalandiridwa ndi mmodzi wa anzanga am’kalasi amene amayi ŵake ali pa njira yamagazini ya amayi ŵanga. Nayenso anatenga chidziŵitso chake m’magazini a Awake! amodzimodziwo.

“Ndikuyamikani kwambiri kaamba ka chidziŵitso chabwino ndi cholongosoka ndiponso chosavuta chimene chimatipanga kukhala anzeru. Mphotho yomwe ndinapata inali unyinji wa 100,000 lire [pafupifupi $100, U.S.], ndipo ndikukutumizirani ndalamazi kuti muzigwiritsire ntchito kusindikiza magazini owonjezereka.”

Tikuganiza kuti mosasamala kanthu za chipembedzo chanu, nanunso mudzapindula ndi nkhani zosangalatsa za mu Galamukani!

Ndingakonde kuti magazini a Galamukani! adzitumizidwa kunyumba kwanga. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena