Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 11/1 tsamba 24
  • Ofunafuna Chowonadi Avomereza Umboni wa Mwamwaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ofunafuna Chowonadi Avomereza Umboni wa Mwamwaŵi
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Khirisimasi?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Krisimasi—kodi Nchifukwa Ninji Iri Yotchuka Kwambiri M’japani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Krisimasi Imatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Chiyambi cha Krisimasi Yamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 11/1 tsamba 24

Lipoti la Olengeza Ufumu

Ofunafuna Chowonadi Avomereza Umboni wa Mwamwaŵi

BAIBULO limatiuza kuti anthu onga nkhosa adzavomereza liwu la Mbusa Wabwino. (Yohane 10:27) Zimenezi ndizo zachitika m’maiko ambiri, kuphatikizapo Briteni.

◻ Mwachitsanzo, mu 1988, itangotsala pang’ono kufika Krisimasi, Pamela, mmodzi wa Mboni za Yehova, anayankha telefoni muofesi mmene ankagwira ntchito nalankhula ndi woimira malonda wogwira ntchito m’kampani imodzimodziyo kumbali ina ya Mangalande. Pamapeto pa kukambitsiranako, mwamunayo anafunsa kuti: “Kodi wakonzekera kale Krisimasi?” Pamela anati: “Ayi!” Wotumiza foniyo anafunsa kuti: “Kodi sunachedwe?” Pamela anayankha kuti: “Sindimakondwerera Krisimasi.” Mwamunayo ananena kuti zimenezo zinali zachilendo ndipo anafunsa chifukwa chake. Pamela anamuuza kuti ali mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo anapitiriza kulongosola kuti m’Baibulo mulibemo lamulo lakukondwerera tsiku lakubadwa kwa Yesu, ndiponso, Yesu sanabadwe pa December 25. Ndiponso, poyambirira Krisimasi inali chikondwerero chachikunja. Wotumiza telefoniyo ananena kuti zonsezo zikumveka zokondweretsa.

Miyezi itatu pambuyo pake Pamela anayankha foni, ndipo wotumizayo anati: “Kodi umakumbukira kuti unalankhula nane isanafike Krisimasi ndipo unandiuza kuti sumakondwerera Krisimasi? Eya, ndachipeza chowonadi!” Anali mwamuna mmodzimodziyo, ndipo analongosola kuti milungu iŵiri pambuyo pa Krisimasi, Mboni ziŵiri zinafika panyumba pake. Anaziitana kuloŵa m’nyumba, ndipo phunziro Labaibulo linayambidwa. Iye anasimba kuti anapanga kupita patsogolo kofulumira m’maphunziro ake. Anauza bwenzi lake lalikazi lomwe anali kukhala nalo kuti njira yawo yamoyo sinali yokondweretsa kwa Yehova, chotero analekana, ndipo tsopano onse aŵiri anali kufikapo pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu.

Kumapeto kwa chakacho, iwo anavomerezedwa monga ofalitsa osabatizidwa, ndipo kuchiyambi kwa 1990 anakwatirana. Ndiyeno anabatizidwa pamodzi. Chotulukapo chabwino koposa cha umboni wamwamwaŵi, wachidule wa pa telefoni!

◻ Yehova anadalitsanso mlongo wina yemwe anachita umboni wamwamwaŵi mu Mangalande. Pamene munthu wa inshuwaransi anafika pakhomo pake, mlongoyo anamfunsa ngati angakonde kutsimikiziridwa za thanzi labwino, chimwemwe, ndi moyo wosatha. Mwamunayo anati inde ndipo anafunsa kuti ndi lamulo la inshuwaransi liti limene anali kunena. Pamene anasonyezedwa m’Baibulo lonjezo la Mulungu la moyo wosatha m’dziko lapansi la Paradaiso, mwamunayo analandira kope la bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndipo anaŵerenga bukhu lonselo madzulo amodzi. Pamene anachezeranso mlongoyo, mwamunayo anamuuza kuti mawuwo anali abwino koposa​—kokha akanakhala ndi chikhulupiriro chomthandiza kuwakhulupirira. Mlongoyo anafotokoza kuti afunikira kuphunzira Baibulo ndi kufika pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu. Phunziro Labaibulo linakonzedwa, ndipo anayamba kufika pamisonkhano. Iye anabatizidwa m’chilimwe cha chaka chimodzimodzicho. Chaka chimodzi chokha pambuyo pake, iye anakwatira mwana wamkazi wa mlongo yemwe poyamba analalikira kwa iye. “Chotero,” akutero mlongoyo, “ndinapindula ponse paŵiri mbale ndi mkamwini kupyolera mu umboni wanga wamwamwaŵi!”

Nzowonadi kuti ofunafuna chowonadi amavomereza pamene chowonadi cha Baibulo chaperekedwa mwa umboni wamwamwaŵi. Monga momwe Yesu ananenera, nkhosa zake zimamva mawu ake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena