Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 3/15 tsamba 31
  • Ulendo Wokapereka Chithandizo ku Ukraine

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulendo Wokapereka Chithandizo ku Ukraine
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 3/15 tsamba 31

Ulendo Wokapereka Chithandizo ku Ukraine

KACHIŴIRINSO malipoti omvetsa chisoni adzaza m’nkhani za nyuzi. Vuto lazachuma, kupereŵera kwa chakudya, ndi njala zikukantha dziko lapansi​—panthaŵiyi m’mbali zina za yomwe kale inali Soviet Union. Posachedwapa, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linapempha ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Denmark kukonza chithandizo cha Mboni zosoŵa ku Ukraine. Kodi abale a ku Denmark amenewo anachitanji?

Iwo anachitapo kanthu panthaŵi yomweyo! Ofesi yanthambi inatumiza mofulumira abale kukagula chakudya chabwino koposa kumisika. Mipingo yonse ya anthu a Yehova mu Denmark inalandira uthenga, kuwadziŵitsa za kusoŵako. Nthambiyo ikusimba kuti: “Mipingo yonse inali yofunitsitsa kuthandiza. Pomalizira pake, tinakhoza kusonyeza umboni wakuti tinamverera chifundo ovutikawo.” Malole aakulu asanu limodzi ndi aang’ono aŵiri pamodzi ndi adilaivala odzifunira 14 anafika panthambi ya Denmark pa Loŵeruka, December 7, 1991. Ogwira ntchito panthambipo anadzaza magalimotowa ndi zakudya zomwe anagula.

Lolemba masana, pa December 9, magalimotowo ananyamuka ulendo wautali wopita ku Ukraine kudzera ku Ulaya. “Chinali chochitika chokhudza mtima pamene banja lonse la Beteli linasonkhana kutsazikana nawo,” inalemba motero nthambiyo. “Pozindikira kuti apaulendo ambiri okapereka chithandizo amaukiridwa, mapemphero athu ambirimbiri anawaperekeza abalewo njira yonse.”

Kuda nkhaŵako kunatha pa December 18. Nthambi ya Denmark inalandira uthenga wakuti magalimotowo anafika mwachisungiko ku Lviv, Ukraine. Abale a ku Ukraine analandira chithandizocho. Anatonthozedwa motani nanga kutsitsa mapaketi olemera makilogalamu 20 okwanira 1,100​—iliyonse yokhala ndi nyama, ufa watirigu, mpunga, suga, ndi zakudya zina! Zonse pamodzi, magalimotowo anapereka zinthu zofunikira zokwanira matani 22. Nthambi ya Denmark inalemba kuti: “Chimwemwe chathu nchachikulu, pamene tikuthokoza Yehova chifukwa cha chitetezo chake ndi kutipatsa mwaŵi umenewu wakupereka chithandizo.”

Akukonzekeranso kutumiza zovala. Nthambiyo ikusimba kuti m’zimenezinso, “yankho la mipingo lakhala lochititsa chidwi.” Yehova ‘amalemeretsadi anthu ake chifukwa cha kuoloŵa manja konse.’ (2 Akorinto 9:11) Nawonso ali ndi chimwemwe chakuya chomwe chimatulukapo m’kupereka kwaulere kwa abale ndi alongo awo. Chotero chikondi chimene amasonyeza chiri chizindikiro cha otsatira a Yesu. (Yohane 13:35) Chikondi choterocho nchosoŵa zedi m’dziko losaukali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena