Ubatizo “Mwa Dzina La”
MAPENDEDWE a zikalata zagubwa zakudziko zakalekale zopezedwa mumchenga wa ku Igupto kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lino kaŵirikaŵiri amamveketsa bwino Malemba Achikristu Achigiriki. Motani? Mwa kulingalira njira imene mawu ena anagwiritsidwira ntchito, timachititsidwa kumvetsetsa molondola bwinopo mawu amodzimodziwo ogwiritsiridwa ntchito m’Malemba.
Chitsanzo chimodzi ndicho kugwiritsira ntchito kwa Yesu mawu akuti “m’dzina la” pamene analamulira ophunzira ake asanakwere kumwamba kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” Kodi Yesu anatanthauzanji?—Mateyu 28:19.
Akatswiri ena apeza kuti m’zolembedwa zakudziko mawu akuti “m’dzina la,” kapena “mwa dzina la” (Kingdom Interlinear), akugwiritsiridwa ntchito ponena za kulipirira “mangawa a aliyense.” Profesala wa zaumulungu Dr. G. Adolf Deissmann anakhulupirira kuti polingalira za umboni wa zikalata zagumbwazo, “lingaliro lalikulu la . . . mawuwo kubatiza mu dzina la Ambuye, kapena kukhulupirira mwa dzina la Mwana wa Mulungu, nlakuti ubatizowo kapena chikhulupiriro chimaphatikizapo kukhala wa Mulungu kapena wa Mwana wa Mulungu.”—Kanyenyewo ngwa Deissmann.
Mokondweretsa, mawu ofananawo anagwiritsiridwa ntchito ndi Ayuda a m’tsiku la Yesu, monga momwe kwafotokozedwera m’bukhu lakuti Theological Dictionary of the New Testament kuti: “Mdulidwe wa wotembenuzidwira kuchiyuda umachitidwa . . . ‘m’dzina la wotembenuzidwayo,’ kumlandira m’Chiyuda. Mdulidwe umenewu umachitika . . . m’dzina la pangano,’ ndiko kuti kumlandira m’pangano.” Mwakutero unansi umayambidwa ndipo wosakhala Myudayo amakhala wotembenuzidwira kuchiyuda mwa ulamuliro wa pangano.
Chotero kwa Mkristu, ubatizo wotsatira kudzipatulira umayambitsa unansi wapafupi ndi Yehova Mulungu, Mwana wake Yesu Kristu, ndi mzimu woyera. Wotembenukayo amazindikira ulamuliro wa aliyense wa iwo m’njira yake yatsopano ya moyo. Talingalirani mmene zimenezi ziliri zowona kwa aliyense wa atatu otchulidwawo.
Mwa kuzindikira ulamuliro wa Mulungu, timayandikira pafupi naye ndi kulowa muunansi ndi iye. (Ahebri 12:9; Yakobo 4:7, 8) Timafikira kukhala chuma cha Mulungu monga akapolo ake, ogulidwa ndi mtengo wa nsembe yadipo ya Yesu Kristu. (1 Akorinto 3:23; 6:20) Mtumwi Paulo anauzanso Akristu a m’zaka za zana loyamba kuti iwo anali a Yesu Kristu, osati a anthu alionse amene angakhale atawabweretsera chowonadi. (1 Akorinto 1:12, 13; 7:23; yerekezerani ndi Mateyu 16:24.) Ubatizo m’dzina la Mwana umatanthauza kuzindikira chenicheni chimenechi, kuvomereza Yesu monga “njira, ndi chowonadi, ndi moyo.”—Yohane 14:6.
Mzimu woyera nawonso ngwofunika muunansi wathu wabwino ndi Yehova ndi Yesu Kristu. Ubatizo m’dzina la mzimu woyera umasonyeza kuti timazindikira mbali ya mzimu m’zochita za Mulungu ndi ife. Timafuna kutsatira chitsogozo chake, osaunyalanyaza kapena kuchita mosemphana nawo, kudodometsa kugwira kwake ntchito kupyolera mwa ife. (Aefeso 4:30; 1 Atesalonika 5:19) Kusakhala munthu kwa mzimu woyera sikumapereka vuto ponena za kugwiritsiridwa ntchito kapena tanthauzo, monga momwedi kugwiritsiridwa ntchito kwa mawuwo “m’dzina la pangano” sikunachitire m’Chiyuda.
Chifukwa cha chimenecho, panthawi ya kudzipatulira ndi ubatizo, tifunikira kusinkhasinkha mwapemphero pa zimene zikuphatikizidwa muunansi wathu watsopano. Kumafunikiritsa kudzigonjetsera kuchifuniro cha Mulungu, chosonyezedwa m’chitsanzo ndi makonzedwe adipo a Yesu Kristu, koti kuchitidwe kupyolera mwa mzimu woyera pamene utsogoza atumiki a Mulungu onse m’chikondi ndi chigwirizano kuzungulira padziko lonse.