Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 8/1 tsamba 32
  • Kufunafuna Chuma Chobisika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Chuma Chobisika
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 8/1 tsamba 32

Kufunafuna Chuma Chobisika

MU 1848 golidi anatumbidwa pamalo ochekera matabwa okhala m’famu ya Sutter, mu California, U.S.A. Pofika 1849 zikwizikwi za anthu anali kuunjikana kumaloko akufuna kukhupuka mofulumira, ndipo kufunafuna golidi kwakukulu koposa m’mbiri ya United States kunali mkati panthaŵiyo. M’chaka chimodzi chokha, doko lapafupi la San Francisco, linakula kuchokera pa tauni yaing’ono kukhala mzinda wa anthu 25,000. Chiyembekezo chakukhupuka kwa panthaŵi imodzi chinakhaladi chikoka champhamvu.

Mfumu Solomo wa Israyeli wakale anadziŵa mmene anthu anakumbira zolimba kufunafuna chuma chobisika, ndipo ananena zimenezi pamene analemba kuti: “Ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu.”​—Miyambo 2:3-5.

Mukhoza kuchita zinthu zambiri ndi golidi ndi siliva, koma mukhoza kuchita zoposa ndi luntha ndi kuzindikira. Zimenezi zidzakuthandizani kupanga zosankha zoyenera, kuthetsa mavuto, kupambana muukwati, ndi kupeza chimwemwe. (Miyambo 2:11, 12) Mofananamo, chidziŵitso chenicheni ndi nzeru zidzakuthandizani kudziŵa Mlengi wanu, kuzindikira zifuno zake, ndi kumvera ndi kumkondweretsa. Golidi sangakupatseni chilichonse cha zinthu zimenezi.

Mawu a Baibulo awa ngowona: “Nzeru ili chinjirizo monga momwe ndalama iliri chinjirizo, koma kuposa kwa chidziŵitso ndi uku: nzeru isungitsa moyo wa mwiniwake.” (Mlaliki 7:12, New International Version) Pamene kuli kwakuti ambiri amakhumbira kulemera panthaŵi imodzi, nkwanzeru chotani nanga kutsegula Baibulo ndi kukumba luntha, kuzindikira, chidziŵitso, ndi nzeru zimene zuli chuma chenicheni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena